Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 2:19 - Buku Lopatulika

19 Ndipo anati iwo, Munthu Mwejipito anatilanditsa m'manja a abusa, natitungiranso madzi okwanira, namwetsa gululi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo anati iwo, Munthu Mwejipito anatilanditsa m'manja a abusa, natitungiranso madzi okwanira, namwetsa gululi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Iwo aja adayankha kuti, “Mwejipito wina ndiye amene watitchinjiriza kwa abusa, ndipo watitungira madzi omwetsa zoŵeta zonsezi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Atsikanawo anayankha kuti, “Mwigupto wina ndiye watilanditsa kwa abusa. Ndiponso anatitungira madzi ndi kumwetsa ziweto zathu.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 2:19
4 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene Yakobo anaona Rakele, mwana wamkazi wa Labani, mlongo wake wa amake, ndi nkhosa za Labani mlongo wake wa amake, Yakobo anayandikira nagubuduza kuuchotsa mwala pachitsime, nazimwetsa zoweta za Labani, mlongo wake wa amake.


Ndipo pamene anthu okhala m'dzikomo, Akanani, anaona maliro a m'dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro aakulu a Aejipito: chifukwa chake dzina la pamenepo linatchedwa Abele-Mizraimu, pali tsidya lija la Yordani.


M'mene anafika kwa Reuwele atate wao, iye anati, Mwabwera msanga bwanji lero?


Ndipo anati kwa ana ake aakazi, Ali kuti iye? Mwamsiyiranji munthuyo? Kamuitaneni, adzadye chakudya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa