Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 2:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo anati kwa ana ake aakazi, Ali kuti iye? Mwamsiyiranji munthuyo? Kamuitaneni, adzadye chakudya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo anati kwa ana ake akazi, Ali kuti iye? Mwamsiyiranji munthuyo? Kamuitaneni, adzadye chakudya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Tsono bambo waoyo adaŵafunsa kuti, “Nanga iyeyo ali kuti? Chifukwa chiyani mwamsiya komweko munthu ameneyo? Pitani mukamuitane, adzadye nao kuno.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Tsono Reueli anafunsa ana ake kuti, “Ndiye ali kuti munthuyo? Chifukwa chiyani mwamusiya? Kamuyitaneni kuti adzadye.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 2:20
12 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzatenga chakudya pang'ono, nimutonthoze mitima yanu; mutatero mudzapitirira, chifukwa mwafika kwa kapolo wanu. Ndipo anati, Chita chomwecho monga momwe wanena.


Ndipo panali pamene Labani anamva mbiri ya Yakobo mwana wa mlongo wake, iye anathamangira kukakomana naye namfungatira, nampsompsona, namlowetsa m'nyumba mwake. Ndipo iye anamfotokozera Labani zinthu zonsezo.


Ndipo Yakobo anapereka nsembe paphiripo, naitana abale ake kuti adye chakudya; ndipo anadya chakudya, nagona paphiripo usiku wonse.


Ndipo anakonzeratu mphatso asanafike Yosefe usana; chifukwa anamva kuti adzadya chakudya pamenepo.


Mlendo sakagona pakhwalala, koma ndinatsegulira wam'njira pakhomo panga.


Pamenepo anamdzera abale ake onse, ndi alongo ake onse, ndi onse odziwana naye kale, nadya naye mkate m'nyumba yake, nampukusira mitu, namtonthoza pa zoipa zonse Yehova anamfikitsirazi; nampatsanso yense ndalama ndi mphete yagolide.


Ndipo anati iwo, Munthu Mwejipito anatilanditsa m'manja a abusa, natitungiranso madzi okwanira, namwetsa gululi.


Ndipo Mose anavomera kukhala naye munthuyo; ndipo anampatsa Mose mwana wake wamkazi Zipora.


wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.


Musaiwale kuchereza alendo; pakuti mwa ichi ena anachereza angelo osachidziwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa