Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 29:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo panali pamene Labani anamva mbiri ya Yakobo mwana wa mlongo wake, iye anathamangira kukakomana naye namfungatira, nampsompsona, namlowetsa m'nyumba mwake. Ndipo iye anamfotokozera Labani zinthu zonsezo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo panali pamene Labani anamva mbiri ya Yakobo mwana wa mlongo wake, iye anathamangira kukakomana naye namfungatira, nampsompsona, namlowetsa m'nyumba mwake. Ndipo iye anamfotokozera Labani zinthu zonsezo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Labani atamva za Yakobe mwana wa mlongo wake, adathamanga kukakumana naye. Adamkumbatira, namumpsompsona, nkupita naye kunyumba. Tsono Yakobe adafotokozera Labani zonse zimene zidachitika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Labani atamva za Yakobo, mwana wa mlongo wake, anafulumira kukakumana naye. Anamukupatira napsompsona, napita naye ku nyumba kwake. Yakobo anafotokozera Labani zonse zinachitika.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 29:13
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Rebeka anali ndi mlongo wake dzina lake Labani; ndipo Labani anathamangira munthuyo kunja ku kasupe.


Ndipo anati, Talowa iwe, wodalitsidwa ndi Yehova; uimiriranji kunjako? Chifukwa kuti ndakonzeratu nyumba, ndi malo a ngamira.


Munthuyo ndipo analowa m'nyumba, namasula ngamira, napatsa ngamira udzu ndi chakudya, ndi madzi akusamba mapazi ake ndi mapazi a iwo amene anali naye.


Ndipo Esau anathamangira kukomana naye namfungatira, nagwa pankhope pake, nampsompsona; ndipo analira iwo.


Ndipo anampsompsona abale ake onse, nalirira iwo; ndipo pambuyo pake abale ake onse anacheza naye.


Ndipo anthu onse anaoloka Yordani, ndi mfumu yomwe inaoloka; ndipo mfumuyo inapsompsona Barizilai nimdalitsa; ndipo iye anabwerera kunka kumalo kwake.


Ndipo Mose anatuluka kukakomana ndi mpongozi wake, nawerama, nampsompsona; nafunsana ali bwanji, nalowa m'hema.


Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Muka kuchipululu kukakomana ndi Mose. Ndipo anamuka, nakomana naye paphiri la Mulungu, nampsompsona.


Sunandipatsa mpsompsono wa chibwenzi; koma uyu sanaleke kupsompsonetsa mapazi anga, chilowere muno Ine.


Ndipo onsewa analira kwambiri, namkupatira Paulo pakhosi pake, nampsompsona,


Mupatsane moni wina ndi mnzake ndi kupsompsonana kopatulika. Mipingo yonse ya Khristu ikupatsani moni.


Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kuchita machawi nthawi ingatayike.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa