Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 31:54 - Buku Lopatulika

54 Ndipo Yakobo anapereka nsembe paphiripo, naitana abale ake kuti adye chakudya; ndipo anadya chakudya, nagona paphiripo usiku wonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

54 Ndipo Yakobo anapereka nsembe paphiripo, naitana abale ake kuti adye chakudya; ndipo anadya chakudya, nagona paphiripo usiku wonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

54 Tsono Yakobe adapereka nsembe paphiripo, naitana anthu ake kuti adzadye chakudya. Atamaliza kudyako, adagona paphiri pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

54 Yakobo anapereka nsembe pa phiri paja, ndipo anayitana abale ake kuti adzadye chakudya. Atadya chakudya anagona pa phiri pomwepo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 31:54
7 Mawu Ofanana  

Ndipo anakula mwanayo naletsedwa kuyamwa: ndipo Abrahamu anakonza madyerero aakulu tsiku lomwe analetsedwa Isaki kuyamwa.


Ndipo anakonzera iwo madyerero, ndipo anadya namwa.


Ndipo iwo anakhala pansi kuti adye chakudya; ndipo anatukula maso ao, nayang'ana, ndipo taonani, ulendo wa Aismaele anachokera ku Giliyadi ndi ngamira zao, zilinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndi mure alinkumuka kutsikira nazo ku Ejipito.


Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anamtengera Mulungu nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo Aroni ndi akulu onse a Israele anadza kudzadya mkate ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu.


Koma kunena za kalonga, iye akhale m'menemo monga kalonga kudya mkate pamaso pa Yehova; alowe kunjira ya kukhonde la chipata, natulukire njira yomweyi.


Ndipo anawayankha nati, Alipo; onani ali m'tsogolo mwanu; fulumirani pakuti wabwera lero kumzinda kuno; popeza lero anthu akuti aphere nsembe pamsanje;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa