Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 2:18 - Buku Lopatulika

M'mene anafika kwa Reuwele atate wao, iye anati, Mwabwera msanga bwanji lero?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

M'mene anafika kwa Reuwele atate wao, iye anati, Mwabwera msanga bwanji lero?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Atsikana atabwerera kwa bambo wao Reuele, bambo waoyo adaŵafunsa kuti, “Bwanji mwabwerako msanga chotere lero?”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Atsikana aja atabwerera kwa abambo awo Reueli, iye anawafunsa kuti, “Chifukwa chiyani lero mwabwera msanga?”

Onani mutuwo



Eksodo 2:18
7 Mawu Ofanana  

Ndipo anati iwo, Munthu Mwejipito anatilanditsa m'manja a abusa, natitungiranso madzi okwanira, namwetsa gululi.


Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wake, wansembe wa ku Midiyani; natsogolera gululo m'tsogolo mwa chipululu, nafika kuphiri la Mulungu, ku Horebu.


Ndipo Mose anabwera namuka kwa Yetero mpongozi wake, nanena naye, Ndimuketu, ndibwerere kunka kwa abale anga amene ali mu Ejipito, ndikaone ngati akali ndi moyo. Ndipo Yetero ananena ndi Mose, Pita bwino.


Ndipo Mose anati kwa Hobabu mwana wa Reuwele Mmidiyani mpongozi wa Mose, Ife tili kuyenda kunka ku malo amene Yehova anati, Ndidzakupatsani awa; umuke nafe, tidzakuchitira zokoma; popeza Yehova wanenera Israele zokoma.


Koma munthu wakukhala wodetsedwa, koma wosadziyeretsa, azimsadza munthuyo pakati pa msonkhano, popeza waipsa malo opatulika a Yehova; sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa.


Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Iyeyo? Anena, Sindidziwa ine.