Ndipo Mose anati, Ndipatuketu, ndikaone chooneka chachikulucho, chitsambacho sichinyeka bwanji.
Eksodo 19:21 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tsika, chenjeza anthu, kuti angapyolere kwa Yehova kudzaona, ndipo angagwe ambiri a iwowa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tsika, chenjeza anthu, kuti angapyolere kwa Yehova kudzaona, ndipo angagwe ambiri a iwowa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adauza Mose kuti, “Tsika pansi, ndipo uza anthu kuti asapitirire malire ndi kubwera kumadzayang'ana kwa Ine, kuti ambiri mwa iwowo angadzafe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo Yehova anati kwa iye, “Tsika ukawachenjeze anthu kuti asayesere kudutsa malire kuti adzandione chifukwa ambiri a iwo adzafa. |
Ndipo Mose anati, Ndipatuketu, ndikaone chooneka chachikulucho, chitsambacho sichinyeka bwanji.
Ndipo Iye anati, Usayandikire kuno; vula nsapato zako ku mapazi ako, pakuti pamalo pamene upondapo iwe, mpopatulika.
Ananenanso, Sungathe kuona nkhope yanga; pakuti palibe munthu adzandiona Ine ndi kukhala ndi moyo.
Samalira phazi lako popita kunyumba ya Mulungu; pakuti kuyandikira kumvera kupambana kupereka nsembe za zitsiru; pakuti sizizindikira kuti zilikuchimwa.
Atatha Aroni ndi ana ake aamuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zake zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'chigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati m'chihema chokomanako.
koma muzitero nao kuti akhale ndi moyo, osafa ai, poyandikiza iwo zopatulika kwambirizo; Aroni ndi ana ake aamuna alowe, namuikire munthu yense ntchito yake ndi katundu wake.
(ndinalinkuima pakati pa Yehova ndi inu muja, kukulalikirani mau a Yehova; popeza munachita mantha chifukwa cha moto, osakwera m'phirimo) ndi kuti:
Ndipo Mulungu anakantha anthu a ku Betesemesi, chifukwa anasuzumira m'likasa la Yehova, anakantha anthu zikwi makumi asanu; ndipo anthu analira maliro, chifukwa Yehova anawakantha anthuwo ndi makanthidwe aakulu.