Eksodo 17:7 - Buku Lopatulika Ndipo anatcha dzina la malowo Masa, ndi Meriba, chifukwa cha kutsutsana kwa ana a Israele; popezanso anayesa Yehova, ndi kuti, Kodi Yehova ali pakati pa ife, kapena iai? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anatcha dzina la malowo Masa, ndi Meriba, chifukwa cha kutsutsana kwa ana a Israele; popezanso anayesa Yehova, ndi kuti, Kodi Yehova ali pakati pa ife, kapena iai? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Malowo adaŵatcha Mayeso ndiponso Makangano, chifukwa Aisraele adakangana ndi Mose, ndipo adayesa Chauta pofunsa kuti, “Kodi Chauta ali nafe, kapena ai?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo iye anatcha malowo Masa ndi Meriba chifukwa Aisraeli anakangana ndi kuyesa Yehova ponena kuti, “Kodi pakati pathu pali Yehova kapena palibe?” |
Unaitana posautsika, ndipo ndinakulanditsa; ndinakuvomereza mobisalika m'bingu; ndinakuyesa kumadzi a Meriba.
Pamenepo anthu anatsutsana ndi Mose, nati, Tipatseni madzi timwe. Koma Mose ananena nao, Mutsutsana nane bwanji? Muyeseranji Yehova?
Ndipo anati, Ngati ndapeza ufulu tsopano pamaso panu, Ambuye, ayendetu Ambuye pakati pa ife; pakuti awa ndi anthu opulupudza; ndipo mutikhululukire mphulupulu ndi uchimo wathu, ndipo mutilandire tikhale cholowa chanu.
Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.
Akulu ake aweruza chifukwa cha mphotho, ndi ansembe ake aphunzitsa chifukwa cha malipo, ndi aneneri ake alosa chifukwa cha ndalama; koma atsamira pa Yehova, nati, Kodi Yehova sali pakati pa ife? Palibe choipa chodzatigwera.
popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikiro zanga, ndidazichita mu Ejipito ndi m'chipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;
Awa ndi madzi a Meriba; popeza ana a Israele anatsutsana ndi Yehova, ndipo anapatulidwa mwa iwowa.
Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake; pakuti sadzalowa m'dziko limene ndapatsa ana a Israele, popeza munapikisana ndi mau anga ku madzi a Meriba.
popeza munapikisana nao mau anga m'chipululu cha Zini, potsutsana nane khamulo, osandipatula Ine pamadziwo pamaso pao. Ndiwo madzi a Meriba mu Kadesi, m'chipululu cha Zini.
Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.
Pamenepo ndidzawapsera mtima tsiku ilo, ndipo ndidzawataya, ndi kuwabisira nkhope yanga, ndipo adzathedwa, ndi zoipa ndi zovuta zambiri zidzawafikira; kotero kuti adzati tsiku lija, Sizitifikira kodi zoipa izi popeza Mulungu wathu sakhala pakati pa ife?
Ndipo za Levi anati, Tumimu ndi Urimu wanu zikhala ndi wokondedwa wanu, amene mudamuyesa mu Masa, amene mudalimbana naye ku madzi a Meriba;
Ndipo Finehasi, mwana wa Eleazara wansembe ananena ndi ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, lero lino tidziwa kuti Yehova ali pakati pa ife, pakuti simunalakwira nacho Yehova; tsopano mwalanditsa ana a Israele m'dzanja la Yehova.