Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 17:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ndipo iye anatcha malowo Masa ndi Meriba chifukwa Aisraeli anakangana ndi kuyesa Yehova ponena kuti, “Kodi pakati pathu pali Yehova kapena palibe?”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

7 Ndipo anatcha dzina la malowo Masa, ndi Meriba, chifukwa cha kutsutsana kwa ana a Israele; popezanso anayesa Yehova, ndi kuti, Kodi Yehova ali pakati pa ife, kapena iai?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo anatcha dzina la malowo Masa, ndi Meriba, chifukwa cha kutsutsana kwa ana a Israele; popezanso anayesa Yehova, ndi kuti, Kodi Yehova ali pakati pa ife, kapena iai?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Malowo adaŵatcha Mayeso ndiponso Makangano, chifukwa Aisraele adakangana ndi Mose, ndipo adayesa Chauta pofunsa kuti, “Kodi Chauta ali nafe, kapena ai?”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 17:7
21 Mawu Ofanana  

Pa madzi a ku Meriba iwo anakwiyitsa Yehova ndipo mavuto anabwera kwa Mose chifukwa cha anthuwo,


Ananyoza Mulungu mwadala pomuwumiriza kuti awapatse chakudya chimene anachilakalaka.


Pa mavuto anu munayitana ndipo ndinakulanditsani, ndinakuyankhani kuchokera mʼmitambo ya mabingu; ndinakuyesani pa madzi a ku Meriba. Sela


“Imvani anthu anga, ndipo ndidzakuchenjezani ngati mungathe kumvetsera, Inu Israeli!


musawumitse mitima yanu monga momwe munachitira pa Meriba, monga munachitira tsiku lija pa Masa mʼchipululu.


Kotero iwo anakangana ndi Mose nati, “Tipatse madzi akumwa.” Mose anayankha kuti, “Chifukwa chiyani mukukangana ndi ine? Chifukwa chiyani mukumuyesa Yehova?”


Iye anati, “Chonde Ambuye, ngati ndapeza chisomo pamaso panu, lolani Ambuye kuti mupite nafe pamodzi. Ngakhale kuti anthuwa ndi nkhutukumve, khululukirani zoyipa ndi machimo athu, ndipo mutenge ife kukhala anthu anu.”


Fuwulani ndi kuyimba mwachimwemwe, inu anthu a ku Ziyoni; pakuti Woyerayo wa Israeli ndi wamkulu pakati panu.”


Atsogoleri ake amalandira chiphuphu kuti aweruze, ansembe ake amalandira malipiro kuti alalikire, ndipo aneneri ake amanenera kuti alandire ndalama. Komatu amatsamira pa Yehova nʼkumanena kuti, “Kodi Yehova sali pakati pathu? Palibe tsoka limene lidzatigwere.”


palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu amene anaona ulemerero wanga ndi zizindikiro zozizwitsa zimene ndinazichita ku Igupto ndi mʼchipululu muno, koma osandimvera ndi kundiyesa kokwanira kakhumi,


Awa anali madzi a ku Meriba, kumene Aisraeli anakangana ndi Yehova ndiponso kumene Yehovayo anadzionetsa yekha kuti ndi Woyera pakati pawo.


“Aaroni adzakakhala ndi anthu a mtundu wake, sadzalowa mʼdziko limene ndapereka kwa Aisraeli, chifukwa nonse munandiwukira motsutsana ndi malamulo anga ku madzi a ku Meriba.


chifukwa pamene anthu anawukira ku madzi a Meriba mʼchipululu cha Zini, inu nonse simunamvere lamulo londilemekeza Ine ngati Woyera pamaso pawo.” (Awa anali madzi a ku Meriba ku Kadesi mʼchipululu cha Zini).


Mawu anasandulika thupi ndipo anakhala pakati pathu. Ife tinaona ulemerero wake, ulemerero wa Iye amene ndi Mwana mmodzi yekhayo wa Atate, wodzaza ndi chisomo ndi choonadi.


Tsiku limenelo Ine ndidzawakwiyira ndi kuwataya. Ndidzawabisira nkhope yanga, ndipo adzawonongedwa. Masautso ambiri ndi zovuta zambiri zidzawagwera, ndipo tsiku limenelo adzafunsa kuti, ‘Kodi masautso awa sanagwere ife chifukwa Yehova Mulungu wathu sali nafe?’


Za fuko la Alevi anati: “Tumimu wanu ndi Urimu ndi za mtumiki wanu wokhulupirika. Munamuyesa ku Masa; munalimbana naye ku madzi a ku Meriba.


Musamuyese Yehova Mulungu wanu monga munachitira ku Masa.


Inu munamukwiyitsanso Yehova ku Tabera, ku Masa ndi ku Kibiroti Hatava.


Ndipo Finehasi wansembe, mwana wa Eliezara anati kwa mafuko a Rubeni, Gadi ndi Manase, “Lero tadziwa kuti Yehova ali nafe chifukwa zimene mwachitazi simunawukire nazo Yehova. Inu mwapulumutsa Aisraeli onse ku chilango cha Yehova.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa