Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni, ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake; anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.
Eksodo 17:4 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anafuulira kwa Yehova, ndi kuti, Ndiwachitenji anthuwa? Atsala pang'ono kundiponya miyala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anafuulira kwa Yehova, ndi kuti, Ndiwachitenji anthuwa? Andilekera pang'ono kundiponya miyala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Mose adapemphera mokweza mau kwa Chauta, adati, “Kodi anthu ameneŵa ndichite nawo chiyani? Iwowo ngokonzeka kundiponya miyala.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, “Kodi ndichite chiyani ndi anthu awa? Iwo atsala pangʼono kundigenda ndi miyala.” |
Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni, ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake; anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ufuuliranji kwa Ine? Lankhula ndi ana a Israele kuti aziyenda.
Ndipo iye anafuulira kwa Yehova; ndipo Yehova anamsonyeza mtengo ndipo anauponya m'madzimo, ndi madzi anasanduka okoma. Pamenepo anawapangira lemba ndi chiweruzo, ndi pomwepa anawayesa;
Ndipo Mose anati kwa Yehova, Munachitiranji choipa mtumiki wanu? Ndalekeranji kupeza ufulu pamaso panu, kuti muika pa ine katundu wa anthu awa onse?
Koma khamu lonse lidati liwaponye miyala. Ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka m'chihema chokomanako kwa ana onse a Israele.
Ndipo Kora anasonkhanitsa khamu lonse mopikisana nao ku khomo la chihema chokomanako; ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka kwa khamu lonse.
Ndipo anafika kumeneko Ayuda kuchokera ku Antiokeya ndi Ikonio; nakopa makamu, ndipo anamponya Paulo miyala, namguzira kunja kwa mzinda; namuyesa kuti wafa.
Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi chisoni, yense chifukwa cha ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wake.