Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 17:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, “Kodi ndichite chiyani ndi anthu awa? Iwo atsala pangʼono kundigenda ndi miyala.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Ndipo Mose anafuulira kwa Yehova, ndi kuti, Ndiwachitenji anthuwa? Atsala pang'ono kundiponya miyala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Mose anafuulira kwa Yehova, ndi kuti, Ndiwachitenji anthuwa? Andilekera pang'ono kundiponya miyala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Apo Mose adapemphera mokweza mau kwa Chauta, adati, “Kodi anthu ameneŵa ndichite nawo chiyani? Iwowo ngokonzeka kundiponya miyala.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 17:4
11 Mawu Ofanana  

Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake, Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake; iwo anayitana Yehova ndipo Iyeyo anawayankha.


Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Chifukwa chiyani ukufuwulira kwa ine? Uwuze Aisraeli aziyenda.


Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, ndipo Yehova anamuonetsa kamtengo. Iye anakaponya mʼmadzimo ndipo madzi anakhala abwino. Kumeneko Yehova anawayikira lamulo ndi maweruziro. Kumenekonso Yehova anawayesa.


Mose anafunsa Yehova kuti, “Chifukwa chiyani mwabweretsa mavuto otere pa mtumiki wanune? Nʼchiyani chimene ndachita choti sichinakusangalatseni mpaka kundisenzetsa katundu wa anthu onsewa?


Koma gulu lonse linayankhula zofuna kuwagenda miyala. Pamenepo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa Aisraeli onse ku tenti ya msonkhano.


Kora atasonkhanitsa omutsatira ake onse amene amatsutsa nawo pa khomo la tenti ya msonkhano, ulemerero wa Yehova unaonekera kwa gulu lonselo.


Ayuda anatolanso miyala kuti amugende Iye,


Pamenepo iwo anatola miyala kuti amugende, koma Yesu anabisala, nachoka mozemba mʼNyumba ya Mulungu.


Kenaka kunabwera Ayuda ena kuchokera ku Antiokeya ndi Ikoniya nakopa gulu la anthu lija. Iwo anamugenda miyala Paulo namukokera kunja kwa mzindawo, kuganiza kuti wafa.


Kodi si dzanja langa linapanga zonsezi?’


Davide anavutika kwambiri mu mtima mwake chifukwa anthu amakamba zoti amuponye miyala popeza aliyense anali ndi chisoni pokumbukira ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anapeza mphamvu mwa Yehova Mulungu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa