Eksodo 17:10 - Buku Lopatulika Ndipo Yoswa anachita monga Mose adanena naye, nayambana ndi Amaleke; ndipo Mose, ndi Aroni, ndi Huri anakwera pamwamba pa chitunda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yoswa anachita monga Mose adanena naye, nayambana ndi Amaleke; ndipo Mose, ndi Aroni, ndi Huri anakwera pamwamba pa chitunda. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yoswa adachitadi monga momwe Mose adalamulira, adatuluka kukamenyana ndi Aamalekewo. Nthaŵi yomweyo Mose, Aroni ndi Huri adakwera pamwamba pa phiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yoswa anachitadi monga Mose anamulamulira. Iye anapita kukamenyana ndi Aamaleki ndipo Mose, Aaroni ndi Huri anapita pamwamba pa phiri. |
Ndipo kunakhala, pamene Mose anakweza dzanja lake Israele anapambana; koma pamene anatsitsa dzanja lake Amaleke anapambana.
Koma manja a Mose analema; ndipo anatenga mwala, nauika pansi pa iye, nakhala pamenepo; ndipo Aroni ndi Huri anagwiriziza manja ake, wina mbali ina, wina mbali ina; ndi manja ake analimbika kufikira litalowa dzuwa.
Ndipo anati kwa akulu, Tilindeni kuno kufikira tidzabwera kwa inu; ndipo taonani, Aroni ndi Huri ali nanu; munthu akakhala ndi mlandu abwere kwa iwowa.
Taona ndaitana ndi kumtchula dzina lake, Bezalele, mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda;
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
Monga Yehova adalamulira Mose mtumiki wake, momwemo Mose analamulira Yoswa; momwemonso anachita Yoswa; sanachotsepo mau amodzi pa zonse Yehova adalamulira Mose.