Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 24:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo anati kwa akulu, Tilindeni kuno kufikira tidzabwera kwa inu; ndipo taonani, Aroni ndi Huri ali nanu; munthu akakhala ndi mlandu abwere kwa iwowa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo anati kwa akulu, Tilindeni kuno kufikira tidzabwera kwa inu; ndipo taonani, Aroni ndi Huri ali nanu; munthu akakhala ndi mlandu abwere kwa iwowa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Iyeyo anali atauza atsogoleri aja kuti, “Batiyembekezani pano, mpaka tidzakupezeni. Aroni ndi Huri muli nawo pompano. Amene akhale ndi milandu, apite kwa iwowo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Apa nʼkuti Mose atawawuza akuluakulu aja kuti, “Mudikire pano mpaka titabweranso. Aaroni ndi Huri ali nanu, aliyense amene ali ndi milandu apite kwa iwo.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 24:14
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anati kwa anyamata ake, Khalani kuno ndi bulu, ine ndi mwanayu tinka uko, ndipo tikapemphera ndi kubweranso kwa inu.


Ndipo Yoswa anachita monga Mose adanena naye, nayambana ndi Amaleke; ndipo Mose, ndi Aroni, ndi Huri anakwera pamwamba pa chitunda.


Koma manja a Mose analema; ndipo anatenga mwala, nauika pansi pa iye, nakhala pamenepo; ndipo Aroni ndi Huri anagwiriziza manja ake, wina mbali ina, wina mbali ina; ndi manja ake analimbika kufikira litalowa dzuwa.


akakhala nao mlandu adza kwa ine, kuti ndiweruze pakati pa munthu ndi mnansi wake, ndi kuti ndiwadziwitse malemba a Mulungu, ndi malamulo ake.


Koma pamene anaona kuti Mose anachedwa kutsika m'phiri, anthuwo anasonkhana kwa Aroni, nanena naye, Ukani, tipangireni milungu yakutitsogolera; pakuti Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m'dziko la Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera.


Ndipo mudzatsika patsogolo pa ine kunka ku Giligala; ndipo, taonani, ndidzatsikira kwa inu kukapereka zopsereza, ndi kuphera nsembe zamtendere. Mutsotsepo masiku asanu ndi awiri kufikira ndikatsikira kwa inu ndi kukudziwitsani chimene mudzachita.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa