Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 17:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ndipo Yoswa anachitadi monga Mose anamulamulira. Iye anapita kukamenyana ndi Aamaleki ndipo Mose, Aaroni ndi Huri anapita pamwamba pa phiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

10 Ndipo Yoswa anachita monga Mose adanena naye, nayambana ndi Amaleke; ndipo Mose, ndi Aroni, ndi Huri anakwera pamwamba pa chitunda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo Yoswa anachita monga Mose adanena naye, nayambana ndi Amaleke; ndipo Mose, ndi Aroni, ndi Huri anakwera pamwamba pa chitunda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Yoswa adachitadi monga momwe Mose adalamulira, adatuluka kukamenyana ndi Aamalekewo. Nthaŵi yomweyo Mose, Aroni ndi Huri adakwera pamwamba pa phiri.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 17:10
9 Mawu Ofanana  

Azuba atamwalira, Kalebe anakwatira Efurata, amene anamuberekera Huri.


Mose ankati akakweza manja ake, Aisraeli amapambana, koma akatsitsa manja akewo Amaleki amapambana.


Manja a Mose atatopa, Aaroni ndi Huri anatenga mwala ndi kuyika pansi ndipo Mose anakhalapo. Aaroni ndi Huri anagwirizitsa manja a Mose wina mbali ina winanso mbali ina. Choncho manja a Mose analimba mpaka kulowa kwa dzuwa.


Apa nʼkuti Mose atawawuza akuluakulu aja kuti, “Mudikire pano mpaka titabweranso. Aaroni ndi Huri ali nanu, aliyense amene ali ndi milandu apite kwa iwo.”


“Taona, ndasankha Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda.


ndi kuwaphunzitsa amvere zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano.”


Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene Ine ndikulamulani.


Amayi ake anati kwa antchito, “Inu muchite chilichonse chimene akuwuzeni.”


Monga momwe Yehova analamulira mtumiki wake Mose, nayenso Mose analamulira Yoswa ndipo Yoswa anachita chilichonse chimene Yehova analamulira Mose.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa