Eksodo 16:6 - Buku Lopatulika Ndipo Mose ndi Aroni ananena ndi ana onse a Israele, Madzulo mudzadziwa kuti Yehova anakutulutsani m'dziko la Ejipito; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose ndi Aroni ananena ndi ana onse a Israele, Madzulo mudzadziwa kuti Yehova anakutulutsani m'dziko la Ejipito; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Mose ndi Aroni adauza Aisraele onse kuti, “Madzulo omwe ano mudzadziŵa kuti ndi Chauta amene adakutulutsani ku Ejipito, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero Mose ndi Aaroni anati kwa Aisraeli onse, “Nthawi yamadzulo inu mudzadziwa kuti ndi Yehova amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto. |
Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anatulutsa ana a Israele m'dziko la Ejipito, monga mwa makamu ao.
nanena nao ana a Israele, Ha? Mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m'dziko la Ejipito, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife chokhuta; pakuti mwatitulutsa kudza nafe m'chipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala.
Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m'mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife chiyani? Simulikudandaulira ife koma Yehova.
Koma pamene anaona kuti Mose anachedwa kutsika m'phiri, anthuwo anasonkhana kwa Aroni, nanena naye, Ukani, tipangireni milungu yakutitsogolera; pakuti Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m'dziko la Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera.
Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawatulutsa m'dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lolimba?
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, tsikatu, pakuti anthu ako udakwera nao kuchokera m'dziko la Ejipito wadziipsa;
Chifukwa chake nena kwa ana a Israele Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aejipito ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo aakulu;
ndipo ndidzalandira inu mukhale anthu anga, ndipo ndidzakhala Ine Mulungu wanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakutulutsa inu pansi pa akatundu a Aejipito.
Ndipo Mose anati, Ndi ichi mudzadziwa kuti Yehova wanditumiza ine kuchita ntchito izi zonse, ndi kuti sizifuma m'mtima mwangamwanga.
Koma Yehova akalenga chinthu chatsopano, ndi nthaka ikayasama pakamwa pake, nikawameza ndi zonse ali nazo, nakatsikira iwo kumanda ali ndi moyo; pamenepo mudzadziwa kuti anthu awa anyoza Mulungu.