Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 32:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, tsikatu, pakuti anthu ako udakwera nao kuchokera m'dziko la Ejipito wadziipsa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, tsikatu, pakuti anthu ako udakwera nao kuchokera m'dziko la Ejipito wadziipsa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Pamenepo Chauta adauza Mose kuti, “Fulumira, tsika phiri, chifukwa anthu ako amene udaŵatsogolera poŵatulutsa ku Ejipito aja, adziipitsa kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Pamenepo Yehova anati kwa Mose, “Tsika msanga, chifukwa anthu ako amene unawatulutsa mʼdziko la Igupto aja adziyipitsa kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 32:7
17 Mawu Ofanana  

Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, monga umo adachitira atate wake Uziya; pokhapo sanalowe mu Kachisi wa Yehova. Koma anthu anachitabe zovunda.


Koma anamsyasyalika pakamwa pao, namnamiza ndi lilime lao.


Ndipo Yehova anati kwa iye, Muka, tsika; nukwere iwe ndi Aroni pamodzi ndi iwe; koma ansembe ndi anthu asapyole kukwera kwa Yehova, angawapasule.


Koma pamene anaona kuti Mose anachedwa kutsika m'phiri, anthuwo anasonkhana kwa Aroni, nanena naye, Ukani, tipangireni milungu yakutitsogolera; pakuti Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m'dziko la Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera.


Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawatulutsa m'dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lolimba?


Ndipo anazilandira ku manja ao, nachikonza ndi chozokotera, nachiyenga mwanawang'ombe; ndipo anati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m'dziko la Ejipito.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, kwera kuchokera kuno, iwe ndi anthu amene unawakweza kuchokera m'dziko la Ejipito, kunka ku dzikolo ndinalumbirira nalo Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzapatsa mbeu zako ilo;


Mtundu wochimwa inu, anthu olemedwa ndi mphulupulu, mbeu yakuchita zoipa, ana amene achita moononga, iwo amsiya Yehova, iwo amnyoza Woyera wa Israele, iwo adana naye nabwerera m'mbuyo.


Masabata makumi asanu ndi awiri alamulidwira anthu a mtundu wako ndi mzinda wako wopatulika, kumaliza cholakwacho, ndi kutsiriza machimo, ndi kutetezera mphulupulu, ndi kufikitsa chilungamo chosalekeza, ndi kukhomera chizindikiro masomphenya ndi zonenera, ndi kudzoza malo opatulika kwambiri.


Anadzivunditsa kwambiri, monga masiku a Gibea; adzakumbukira mphulupulu yao, adzalanga zochimwa zao.


Pakuti ndidziwa kuti nditamwalira ine mudzadziipsa ndithu, ndi kupatuka m'njira imene ndinakuuzani; ndipo chidzakugwerani choipa masiku otsiriza; popeza mudzachita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake ndi ntchito za manja anu.


Anamchitira zovunda si ndiwo ana ake, chilema nchao; iwo ndiwo mbadwo wopulukira ndi wokhotakhota.


kuti mungadziipse, ndi kudzipangira fano losema, lakunga chifaniziro chilichonse, mafanidwe a mwamuna kapena mkazi;


Ndipo Yehova anati kwa ine, Uka, fulumira kutsika kuno popeza anthu ako unawatulutsa mu Ejipitowa anadziipsa; anapatuka msanga m'njira ndinawalamulirayi; anadzipangira fano loyenga.


Mu Horebu momwe munautsa mkwiyo wa Yehova; ndipo Yehova anakwiya nanu kukuonongani.


Koma kunali atafa woweruzayo anabwerera m'mbuyo, naposa makolo ao ndi kuchita moipitsa, ndi kutsata milungu ina kuitumikira ndi kuigwadira, sanaleke kanthu ka machitidwe ao kapena ka njira yao yatcheni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa