Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 32:8 - Buku Lopatulika

8 wapatuka msanga njira imene ndinawauza; wadzinyengera mwanawang'ombe, namgwadira, namphera nsembe, nati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 wapatuka msanga njira imene ndinawauza; wadzinyengera mwanawang'ombe, namgwadira, namphera nsembe, nati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Asiya mwamsanga zonse zija zimene ndidaŵalamula kuti azichita. Adzipangira fano la mwanawang'ombe wa golide wosungunula, ndipo alipembedza ndi kuliphera nsembe, namanena kuti, ‘Inu Aisraele, nayi milungu yanu imene idakutulutsani ku Ejipito.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Iwo apatuka mwamsanga kuleka kutsatira zimene ndinawalamula. Ndiye adzipangira fano la mwana wangʼombe. Aligwadira ndi kuliperekera nsembe nʼkumati, ‘Inu Aisraeli, nayu mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 32:8
18 Mawu Ofanana  

Potero mfumu inakhala upo, napanga anaang'ombe awiri agolide, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisraele inu milungu yanu, imene inakutulutsani m'dziko la Ejipito.


Ngakhale apa atadzipangira mwanawang'ombe woyenga, nati, Suyu Mulungu wako anakukweza kuchokera ku Ejipito, nachita zopeputsa zazikulu;


Anapanga mwanawang'ombe ku Horebu, nagwadira fano loyenga.


Koma anamsyasyalika pakamwa pao, namnamiza ndi lilime lao.


Musapange milungu yasiliva ikhale pamodzi ndi Ine; musadzipangire milungu yagolide.


Wakuphera nsembe mulungu wina, wosati Yehova yekha, aonongeke konse.


Ndipo anazilandira ku manja ao, nachikonza ndi chozokotera, nachiyenga mwanawang'ombe; ndipo anati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m'dziko la Ejipito.


ungachite pangano ndi iwo okhala m'dzikomo; ndipo angachite chigololo pakutsata milungu yao, nangaphere nsembe milungu yao, ndipo angakuitane wina, nukadye naye nsembe zake;


Amene ataya golide, namtulutsa m'thumba, ndi kuyesa siliva ndi muyeso, iwo alemba wosula golide; iye napanga nazo mulungu; iwo agwada pansi, inde alambira.


si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo ao tsiku lija ndinawagwira manja kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyao, ati Yehova.


Ndipo asamapheranso milungu ina nsembe zao, zimene azitsata ndi chigololo. Ili liwakhalire lemba losatha mwa mibadwo yao.


Anaziphera nsembe ziwanda, si ndizo Mulungu ai; milungu yosadziwa iwo, yatsopano yofuma pafupi, imene makolo anu sanaiope.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Uka, fulumira kutsika kuno popeza anthu ako unawatulutsa mu Ejipitowa anadziipsa; anapatuka msanga m'njira ndinawalamulirayi; anadzipangira fano loyenga.


Ndipo ndinapenya, taonani, mudachimwira Yehova Mulungu wanu; mudadzipangira mwanawang'ombe woyenga; mudapatuka msanga m'njira imene Yehova adalamulira inu.


M'mene anafika kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase, ku dziko la Giliyadi, ananena nao ndi kuti,


Koma sanamvere angakhale oweruza ao, pakuti anamuka kupembedza milungu ina, naigwadira; anapatuka msanga m'njira yoyendamo makolo ao, pomvera malamulo a Yehova; sanatero iwowa.


Gideoni anatinso kwa iwo, Mundilole ndipemphe kanthu kamodzi kwa inu, mundipatse aliyense maperere mwa zofunkha zanu; pakuti anali nao maperere agolide, pokhala anali Aismaele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa