Eksodo 32:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo m'mawa mwake anauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, nabwera nazo nsembe zamtendere; ndi anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kusewera. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo m'mawa mwake anauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, nabwera nazo nsembe zamtendere; ndi anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kusewera. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Choncho m'maŵa mwake, m'mamaŵa ndithu, adapereka nsembe zopsereza, nabweranso ndi nsembe zamtendere. Ndipo anthuwo adakhala pansi nayamba kudya ndi kumwa, kenaka adayambanso kuvina. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Kotero tsiku linalo anthu anadzuka mmamawa ndithu ndi kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Atatha kupereka nsembezo, anthuwo anakhala pansi nayamba kudya ndi kumwa. Kenaka anayimirira nayamba kuvina mwachilendo. Onani mutuwo |