Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 32:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Kotero tsiku linalo anthu anadzuka mmamawa ndithu ndi kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Atatha kupereka nsembezo, anthuwo anakhala pansi nayamba kudya ndi kumwa. Kenaka anayimirira nayamba kuvina mwachilendo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

6 Ndipo m'mawa mwake anauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, nabwera nazo nsembe zamtendere; ndi anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kusewera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo m'mawa mwake anauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, nabwera nazo nsembe zamtendere; ndi anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kusewera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Choncho m'maŵa mwake, m'mamaŵa ndithu, adapereka nsembe zopsereza, nabweranso ndi nsembe zamtendere. Ndipo anthuwo adakhala pansi nayamba kudya ndi kumwa, kenaka adayambanso kuvina.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 32:6
10 Mawu Ofanana  

Aaroni ataona izi, anamanga guwa lansembe patsogolo pa mwana wangʼombeyo ndipo analengeza kuti, “Mawa kudzakhala chikondwerero cha Yehova.”


Anthuwo amakagonana mʼmbali mwa guwa lililonse la nsembe pa zovala zimene anatenga ngati chikole. Mʼnyumba ya mulungu wawo amamweramo vinyo amene analipiritsa anthu pa milandu.


Maphwando anu achipembedzo ndidzawasandutsa kulira kwa chisoni ndipo kuyimba kwanu konse ndidzakusandutsa maliro. Ndidzakuvekani chiguduli nonsenu ndi kumeta mipala mitu yanu. Nthawi imeneyo idzakhala ngati yolira mwana wamwamuna mmodzi yekhayo, ndipo tsikulo lidzakhala lowawa mpaka kutha kwake.


amene ankawayitana ku nsembe za milungu yawo. Anthuwo anadya chakudya chopereka kwa milungu ndi kupembedza milunguyo.


Musakhale anthu opembedza mafano, monga analili ena mwa iwo. Pakuti zalembedwa kuti, “Anthuwo anakhala pansi nayamba kudya ndi kumwa. Kenaka anayimirira nayamba kuvina mwachilendo.”


Anthu okhala pa dziko lapansi adzasangalala nazo zimenezi. Adzachita chikondwerero ndi kutumizirana mphatso, chifukwa aneneri awiri amenewa ankasautsa anthu okhala pa dziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa