Eksodo 32:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Pamenepo Yehova anati kwa Mose, “Tsika msanga, chifukwa anthu ako amene unawatulutsa mʼdziko la Igupto aja adziyipitsa kwambiri. Onani mutuwoBuku Lopatulika7 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, tsikatu, pakuti anthu ako udakwera nao kuchokera m'dziko la Ejipito wadziipsa; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, tsikatu, pakuti anthu ako udakwera nao kuchokera m'dziko la Ejipito wadziipsa; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Pamenepo Chauta adauza Mose kuti, “Fulumira, tsika phiri, chifukwa anthu ako amene udaŵatsogolera poŵatulutsa ku Ejipito aja, adziipitsa kwambiri. Onani mutuwo |
“Zaka 490 zinayikidwa kuti anthu a mtundu wako ndi mzinda wanu woyera aleke zoyipa, asiye tchimo. Iwo adzapereka dipo kupepesera zolakwa zawo. Zikadzatero anthu adzaonetsa moyo wachilungamo nthawi zonse. Izi zidzatsimikiza zimene unaziona mʼmasomphenya zija ndi zimene ananenera aneneri. Malo opatulika adzakhazikitsidwa.