Eksodo 12:42 - Buku Lopatulika Ndiwo usiku wosungira Yehova ndithu, chifukwa cha kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; usiku womwe uno ukhale wosungira Yehova ana onse a Israele ku mibadwo yao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiwo usiku wosungira Yehova ndithu, chifukwa cha kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; usiku womwe uno ukhale wosungira Yehova ana onse a Israele ku mibadwo yao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Usiku wonse Chauta adachezera kutulutsa Aisraelewo m'dziko lija la Ejipito. Nchifukwa chake usiku umenewu ndi wopatulikira Chauta pa mibadwo yonse, kuti ukhale usiku womwe Aisraele onse ayenera kuchezera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Usiku wonse Yehova anachezera kutulutsa ana a Israeli mʼdziko la Igupto. Nʼchifukwa chake pa tsiku limeneli Aisraeli onse azichezera usiku wonse kulemekeza Mulungu kamba ka mibado yonse ya mʼtsogolo. |
Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.
Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku lino limene munatuluka mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo; pakuti Yehova anakutulutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka chotupitsa.
Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa. Uzidya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri, monga ndakuuza pa nthawi yonenedwa, m'mwezi wa Abibu; pakuti mwezi wa Abibu unatuluka mu Ejipito.