Analambulira mkwiyo wake njira; sanalekerere moyo wao usafe, koma anapereka moyo wao kumliri.
Eksodo 12:30 - Buku Lopatulika Ndipo Farao anauka usiku, iye ndi anyamata ake onse ndi Aejipito onse; ndipo kunali kulira kwakukulu mu Ejipito; pakuti panalibe nyumba yopanda wakufa m'mwemo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Farao anauka usiku, iye ndi anyamata ake onse ndi Aejipito onse; ndipo kunali kulira kwakukulu m'Ejipito; pakuti panalibe nyumba yopanda wakufa m'mwemo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Farao ndi nduna zake zonse, pamodzi ndi Aejipito onse, adadzuka pakati pa usiku, ndipo m'dziko lonse la Ejipito munali maliro okhaokha, chifukwa panalibe banja lopanda mwana wakufa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Farao ndi nduna zake zonse ndiponso Aigupto onse anadzuka pakati pa usiku, ndipo kunali kulira kwakukulu mʼdziko lonse la Igupto, pakuti panalibe nyumba imene munalibe munthu wakufa. |
Analambulira mkwiyo wake njira; sanalekerere moyo wao usafe, koma anapereka moyo wao kumliri.
Ndipo ananena nao, Momwemo, Yehova akhale nanu ngati ndilola inu ndi ana aang'ono anu mumuke; chenjerani pakuti pali choipa pamaso panu.
Ndipo kudzakhala kulira kwakukulu m'dziko lonse la Ejipito, kunalibe kunzake kotere, sikudzakhalanso kunzake kotere.
Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.
Ndipo amene anapanda kufa anagwidwa ndi mafundowo; ndi kulira kwa mzindawo kunakwera kumwamba.