Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Amosi 5:17 - Buku Lopatulika

17 Ndi m'minda yonse yamipesa mudzakhala kulira, pakuti ndipita pakati pako, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndi m'minda yonse yamipesa mudzakhala kulira, pakuti ndipita pakati pako, ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 M'minda yonse ya mphesa mudzakhala kulira kokhakokha, pakuti ndidzakulanganidi nonsenu.” Akuterotu Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Mʼminda yonse ya mpesa mudzakhala kulira kokhakokha, pakuti Ine ndidzadutsa pakati panu,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 5:17
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Mose anati, Atero Yehova, Monga pakati pa usiku ndidzatuluka Ine kunka pakati pa Aejipito;


Pakuti ndidzapita pakati padziko la Ejipito usiku womwewo, ndi kukantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito, anthu ndi zoweta; ndipo ndidzachita maweruzo pa milungu yonse ya Aejipito; Ine ndine Yehova.


Pakuti Yehova adzapita pakatipo kukantha Aejipito; koma pamene adzaona mwaziwo pa mphuthu pamwamba ndi za pambali, Yehova adzapitirira pakhomopo, osalola woononga alowe m'nyumba zanu kukukanthani.


Ndipo chikondwerero ndi msangalalo zachotsedwa m'munda wopatsa zipatso; ndi m'minda ya mipesa simudzakhala kuimba, ngakhale phokoso losangalala; palibe woponda adzaponda vinyo m'moponderamo; ndaleketsa mfuu wa masika amphesa.


Ndipo kusekera ndi kukondwa kwachotsedwa, kumunda wobala ndi kudziko la Mowabu; ndipo ndaletsa vinyo pa zoponderamo; sadzaponda ndi kufuula; kufuula sikudzakhala kufuula.


Momwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu wakukhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika; pamenepo Yerusalemu adzakhala wopatulika, osapitanso alendo pakati pake,


Atero Yehova: Angakhale iwo ali ndi mphamvu yokwanira, nachuluka momwemo, koma momwemonso adzasalikidwa, ndipo iye adzapitiratu. Chinkana ndakuzunza iwe, sindidzakuzunzanso.


Taonani pamapiri mapazi a iye wakulalikira uthenga wabwino, wakubukitsa mtendere! Chita chikondwerero chako, Yuda, kwaniritsa zowinda zako; pakuti wopanda pakeyo sadzapitanso mwa iwe; iye waonongeka konse.


Ndipo ndidzamangira nyumba yanga misasa, kuiletsera nkhondo, asapitepo munthu kapena kubweranso; ndipo wakuwasautsa sadzapitanso pakati pao; pakuti tsopano ndapenya ndi maso anga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa