Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 12:19 - Buku Lopatulika

Chisapezeke chotupitsa m'nyumba zanu masiku asanu ndi awiri; pakuti aliyense wakudya kanthu ka chotupitsa, munthuyo adzachotsedwa ku gulu la Israele, angakhale ndiye mlendo kapena wobadwa m'dziko.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Chisapezeke chotupitsa m'nyumba zanu masiku asanu ndi awiri; pakuti aliyense wakudya kanthu ka chotupitsa, munthuyo adzasadzidwa ku msonkhano wa Israele, angakhale ndiye mlendo kapena wobadwa m'dziko.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pa masiku asanu ndi aŵiri onsewo, m'nyumba mwanu musadzapezeke chofufumitsira buledi, chifukwa wina aliyense akadzadya chakudya chofufumitsa, adzachotsedwa pa mtundu wa Aisraele, mlendo ngakhale mbadwa yomwe.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yisiti asamapezeka mʼnyumba zanu kwa masiku asanu ndi awiri. Ndipo aliyense amene adya chakudya chimene muli yisiti, munthu ameneyo ayenera kuchotsedwa mʼgulu la Aisraeli, kaya iyeyo ndi mlendo kapena mbadwa.

Onani mutuwo



Eksodo 12:19
13 Mawu Ofanana  

Masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa; lingakhale tsiku loyamba muzichotsa chotupitsa m'nyumba zanu; pakuti aliyense wakudya mkate wa chotupitsa kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lachisanu ndi chiwiri, munthu ameneyo adzachotsedwa kwa Israele.


Musadye kanthu ka chotupitsa; mokhala inu monse muzidya mkate wopanda chotupitsa.


Ndipo Yehova anati kwa Mose ndi Aroni, Lemba la Paska ndi ili: mwana wa mlendo aliyense asadyeko;


Koma akakhala nanu mlendo, nakonzera Yehova Paska, adulidwe amuna ake onse, ndipo pamenepo asendere kuuchita; nakhale ngati wobadwa m'dziko; koma wosadulidwa aliyense asadyeko.


Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku lino limene munatuluka mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo; pakuti Yehova anakutulutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka chotupitsa.


Azikadya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiriwo ndipo kasaoneke kanthu ka chotupitsa kwanu; inde chotupitsa chisaoneke kwanu m'malire ako onse.


Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda chotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unatuluka mu Ejipito; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu;


Aliyense amene akonza ena otere, kapena aliyense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wake.


Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa. Uzidya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri, monga ndakuuza pa nthawi yonenedwa, m'mwezi wa Abibu; pakuti mwezi wa Abibu unatuluka mu Ejipito.


Mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo, pali Paska wa Yehova.


Munthu akakhala woyera, wosakhala paulendo, koma akaleka kuchita Paska, amsadze munthuyo kwa anthu a mtundu wake; popeza sanabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, munthuyu asenze kuchimwa kwake.


Musamadyera nayo mkate wa chotupitsa; masiku asanu ndi awiri mudyere nayo mkate wopanda chotupitsa, ndiwo mkate wa chizunziko popeza munatuluka m'dziko la Ejipito mofulumira; kuti mukumbukire tsiku lotuluka inu m'dziko la Ejipito masiku onse a moyo wanu.