Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 1:12 - Buku Lopatulika

Koma monga momwe anawasautsiramo, momwemo anachuluka, momwemonso anafalikira. Ndipo anavutika chifukwa cha ana Israele.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma monga momwe anawasautsiramo, momwemo anachuluka, momwemonso anafalikira. Ndipo anavutika chifukwa cha ana Israele.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma Aisraele ankati akamaŵazunza kwambiri, ndi pamene iwo tsono ankachulukirachulukira, mpaka adabalalikira m'dziko lonselo. Motero Aejipito ankaŵaopa Aisraele,

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma pamene ankawazunza kwambiri, Aisraeli ndiye ankachulukirachulukira mpaka kubalalikira mʼdziko lonse. Kotero Aigupto anayamba kuopa Aisraeliwo

Onani mutuwo



Eksodo 1:12
17 Mawu Ofanana  

Nati iye, Ndine pano. Ndipo anati, Ine ndine Mulungu, Mulungu wa atate wako; usaope kunka ku Ejipito; pakuti pamenepo ndidzakusandutsa iwe mtundu waukulu;


Ana aonso munawachulukitsa monga nyenyezi za m'mwamba, nimunawalowetsa m'dziko mudalinena kwa makolo ao, alowemo likhale laolao.


Pakuti mkwiyo umapha wopusa, ndi nsanje imakantha wopanda pake.


Ndipo anachulukitsatu mtundu wa anthu ake, nawapatsa mphamvu yoposa owasautsa.


Ndipo awadalitsa, kotero kuti achuluka kwambiri; osachepsanso zoweta zao.


Potero Mulungu anawachitira zabwino anamwino; ndipo anthuwo anachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu.


Ana a Israele ndipo anaswana, nabalana, nachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu; ndipo dziko linadzala nao.


Ndipo ananena ndi anthu ake, Taonani, anthu, ndiwo ana a Israele, achuluka, natiposa mphamvu.


Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.


Kupweteka mtima nkwa nkhanza, mkwiyo usefuka; koma ndani angalakike ndi nsanje?


Ndipo Mowabu anachita mantha akulu ndi anthuwo, popeza anachuluka; nada mtima Mowabu chifukwa cha ana a Israele.


Chifukwa chake Afarisi ananena wina ndi mnzake, Muona kuti simupindula kanthu konse; onani dziko litsata pambuyo pake pa Iye.


Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.


Ndipo muyankhe ndi kuti pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Kholo langa ndiye Mwaramu wakuti atayike, natsika kunka ku Ejipito, nagoneragonera komweko ali nao anthu pang'ono, nasandukako mtundu waukulu, wamphamvu, ndi wochuluka anthu ake;