Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 9:23 - Buku Lopatulika

23 Ana aonso munawachulukitsa monga nyenyezi za m'mwamba, nimunawalowetsa m'dziko mudalinena kwa makolo ao, alowemo likhale laolao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ana aonso munawachulukitsa monga nyenyezi za m'mwamba, nimunawalowetsa m'dziko mudalinena kwa makolo ao, alowemo likhale laolao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Mudachulukitsa zidzukulu zao ngati nyenyezi zamumlengalenga. Mudaŵaloŵetsa m'dziko limene mudaauza makolo ao kuti adzalilandira nkukhala lao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Munachulukitsa ana awo aamuna ngati nyenyezi za mlengalenga. Ndipo munawabweretsa mʼdziko limene munawuza makolo awo kuti alilowe ndi kulitenga.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 9:23
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.


Tsiku lomwelo Yehova anapangana chipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pamtsinje wa ku Ejipito kufikira pamtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate:


Ndipo anamtulutsa iye kunja, nati, Tayang'anatu kumwamba, uwerenge nyenyezi, ngati ukhoza kuziwerenga zimenezo: ndipo anati kwa iye, Zoterezo zidzakhala mbeu zako.


Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la Kanani likhale lako nthawi zonse: ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wako.


kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa chipata cha adani ao;


khala mlendo m'dziko muno, ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndipo ndidzadalitsa iwe chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako maiko onse awa, ndipo ndidzalimbikitsa chilumbiriro ndinachilumbirira kwa Abrahamu atate wako;


Koma Davide sanawerenge iwo a zaka makumi awiri ndi ochepapo, pakuti Yehova adati kuti adzachulukitsa Israele ngati nyenyezi za kuthambo.


Koma monga momwe anawasautsiramo, momwemo anachuluka, momwemonso anafalikira. Ndipo anavutika chifukwa cha ana Israele.


Ana a Israele ndipo anaswana, nabalana, nachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu; ndipo dziko linadzala nao.


Ndipo mudzatsala anthu pang'ono, mungakhale mudachuluka ngati nyenyezi za m'mwamba; popeza simunamvere mau a Yehova Mulungu wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa