Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 9:22 - Buku Lopatulika

22 Munawapatsanso maufumu, ndi mitundu ya anthu, nimunawagawa m'madera, motero analandira likhale laolao dziko la Sihoni, ndilo dziko la mfumu ya ku Hesiboni, ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Munawapatsanso maufumu, ndi mitundu ya anthu, nimunawagawa m'madera, motero analandira likhale laolao dziko la Sihoni, ndilo dziko la mfumu ya ku Hesiboni, ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Mudaŵapatsa mphamvu zogonjetsera maiko ndiponso mitundu ya anthu. Mudaŵagaŵiranso maiko achilendo, ndipo choncho adalanda dziko la Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 “Inu munawapatsa mafumu ndi mayiko mʼmanja mwawo. Munawagawiranso mayiko achilendo akutali kwambiri. Munabwera nawo mʼdziko la Sihoni mfumu ya Hesiboni ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani kuti alowemo nʼkulitenga kukhala lawo.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 9:22
16 Mawu Ofanana  

Ndipo anawapatsa maiko a amitundu; iwo ndipo analanda zipatso za ntchito ya anthu:


Pamenepo Ambuye anauka ngati wam'tulo; ngati chiphona chakuchita nthungululu ndi vinyo.


Ine ndinalenga dziko lapansi, anthu ndi nyama zokhala m'dzikomo, ndi mphamvu yanga yaikulu ndi mkono wanga wotambasuka; ndipo ndinapereka ilo kwa iye amene ayenera pamaso panga.


ndipo analowa, nakhalamo; koma sanamvere mau anu, sanayende m'chilamulo chanu; sanachite kanthu ka zonse zimene munawauza achite; chifukwa chake mwafikitsa pa iwo choipa chonsechi;


Nditafika nao m'dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya chitunda chilichonse chachitali, ndi mtengo uliwonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, naperekapo nsembe zao zondiputa, aponso anachita fungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira.


atakantha Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala mu Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basani, wakukhala mu Asitaroti, ku Ederei.


Ndinati, Ndikadawauzira ndithu, ndikadafafaniza chikumbukiro chao mwa anthu.


tsidya lija la Yordani, m'chigwa cha pandunji pa Betepeori, m'dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala mu Hesiboni, amene Mose ndi ana a Israele anamkantha, potuluka iwo mu Ejipito;


ndipo analanda dziko lake, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, mafumu awiri a Aamori, akukhala tsidya lija la Yordani lotuluka dzuwa;


Ndipo kunali, pakuthawa iwo pamaso pa Israele, potsikira pa Betehoroni, Yehova anawagwetsera miyala yaikulu yochokera kumwamba mpaka pa Azeka, nafa iwo; akufa ndi miyala yamatalala anachuluka ndi iwo amene ana a Israele anawapha ndi lupanga.


Motero Yoswa analanda dziko lonse monga mwa zonse Yehova adazinena kwa Mose; ndipo Yoswa analipereka kwa Israele, likhale cholowa chao, fuko lililonse gawo lake. Ndipo dziko linapumula nkhondo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa