Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 9:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo munawalera zaka makumi anai m'chipululu, osasowa kanthu iwo; zovala zao sizinathe, ndi mapazi ao sanatupe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo munawalera zaka makumi anai m'chipululu, osasowa kanthu iwo; zovala zao sizinatha, ndi mapazi ao sanatupe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Mudaŵasunga zaka makumi anai m'chipululu ndipo nthaŵi yonseyo sankasoŵa kanthu. Zovala zao sizidathe, mapazi aonso sadatupe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Munawasunga zaka makumi anayi mʼchipululu ndipo sanasowe kanthu kalikonse. Zovala zawo sizinathe kapena mapazi awo kutupa.”

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 9:21
9 Mawu Ofanana  

Misona ya mkango isowa nimva njala, koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino.


Ndipo ana a Israele anadya mana zaka makumi anai, kufikira atalowa dziko la midzi; anadya mana kufikira analowa malire a dziko la Kanani.


Ngati munabwera nazo kwa Ine nsembe zophera ndi zaufa zaka makumi anai m'chipululu, inu nyumba ya Israele?


Ndipo monga nthawi ya zaka makumi anai anawalekerera m'chipululu.


Pakuti Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mu ntchito zonse za manja anu; anadziwa kuyenda kwanu m'chipululu ichi chachikulu; zaka izi makumi anai Yehova Mulungu wanu anakhala ndi inu; simunasowe kanthu.


Ndipo ndinakutsogolerani zaka makumi anai m'chipululu; zovala zanu sizinathe pathupi panu, ndi nsapato zanu sizinathe pa phazi lanu.


Ndipo mukumbukire njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m'chipululu zaka izi makumi anai, kuti akuchepetseni, kukuyesani, kudziwa chokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ake, kapena iai.


Zovala zanu sizinathe pathupi panu, phazi lanu silinatupe zaka izi makumi anai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa