Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 12:19 - Buku Lopatulika

19 Chifukwa chake Afarisi ananena wina ndi mnzake, Muona kuti simupindula kanthu konse; onani dziko litsata pambuyo pake pa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Chifukwa chake Afarisi ananena wina ndi mnzake, Muona kuti simupindula kanthu konse; onani dziko litsata pambuyo pake pa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Pamenepo Afarisi adayamba kuuzana kuti, “Mukuwonatu kuti sitikuphulapo kanthu konse. Onani anthu onse akumthamangira.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Choncho Afarisi anati kwa wina ndi mnzake, “Taonani, palibe chimene mwachitapo. Anthu onse akumutsatira Iye!”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 12:19
14 Mawu Ofanana  

Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Yehova, ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.


Dzamveni kuno, anthu inu nonse; tcherani khutu, inu nonse amakono,


M'mibadwo ikudzayo Yakobo adzamera mizu; Israele adzaphuka ndi kuchita mphundu; ndipo iwo adzadzaza ndi zipatso padziko lonse lapansi.


Koma ansembe aakulu ndi alembi, m'mene anaona zozizwitsa zomwe Iye anazichita, ndi ana alinkufuula ku Kachisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide, anapsa mtima,


Chifukwa cha ichinso khamulo linadza kudzakomana ndi Iye, chifukwa anamva kuti Iye adachita chizindikiro ichi.


Koma panali Agriki ena mwa iwo akukwera kunka kukalambira pachikondwerero.


kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa Ife: kuti dziko lapansi likakhulupirire kuti Inu munandituma Ine.


Ndipo anadza kwa Yohane, nati kwa iye, Rabi, Iye amene anali ndi inu tsidya lija la Yordani, amene munamchitira umboni, taonani yemweyu abatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa Iye.


Pamene sanawapeze anakokera Yasoni ndi abale ena pamaso pa akulu a mzinda, nafuula kuti, Omwe aja asanduliza dziko lokhalamo anthu, afika kunonso;


ndipo Iye ndiye chiombolo cha machimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa