Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 9:1 - Buku Lopatulika

Chaka choyamba cha Dariusi mwana wa Ahasuwero, wa mbeu ya Amedi, amene anamlonga mfumu ya Ababiloni;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Chaka choyamba cha Dariusi mwana wa Ahasuwero, wa mbeu ya Amedi, amene anamlonga mfumu ya Ababiloni;

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mʼchaka choyamba cha Dariyo mwana wa Ahasiwero (wochokera kwa Amedi), amene anakhala mfumu ya ku Babuloni,

Onani mutuwo



Danieli 9:1
9 Mawu Ofanana  

Ndipo pokhala mfumu Ahasuwero, poyambira ufumu wake, analembera chowaneneza okhala mu Yuda ndi mu Yerusalemu.


Izi zinachitika masiku a Ahasuwero, ndiye Ahasuweroyo anachita ufumu kuyambira Indiya kufikira Kusi, pa maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri.


Nakhala moyo Daniele mpaka chaka choyamba cha mfumu Kirusi.


anyamata opanda chilema, a maonekedwe okoma, a luso la nzeru zonse, ochenjera m'kudziwa, a luntha lakuganizira, okhoza kuimirira m'chinyumba cha mfumu; ndi kuti awaphunzitse m'mabuku, ndi manenedwe a Ababiloni.


Ndipo ine, chaka choyamba cha Dariusi Mmedi, ndinauka kumlimbikitsa ndi kumkhazikitsa.


Ndipo Dariusi Mmedi analandira ufumuwo ali wa zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri.


Kudamkomera Dariusi kuikira ufumuwo akalonga zana limodzi mphambu makumi awiri akhale m'madera onse a ufumu;


Momwemo Daniele amene anakuzikabe pokhala Dariusi mfumu, ndi pokhala mfumu Kirusi wa ku Persiya.