Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 9:2 - Buku Lopatulika

2 chaka choyamba cha ufumu wake, ine Daniele ndinazindikira mwa mabuku kuti chiwerengo chake cha zaka, chimene mau a Yehova anadzera nacho kwa Yeremiya mneneri, kunena za makwaniridwe a mapasuko a Yerusalemu, ndizo zaka makumi asanu ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 chaka choyamba cha ufumu wake, ine Daniele ndinazindikira mwa mabuku kuti chiwerengo chake cha zaka, chimene mau a Yehova anadzera nacho kwa Yeremiya mneneri, kunena za makwaniridwe a mapasuko a Yerusalemu, ndizo zaka makumi asanu ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 ine Danieli ndinazindikira powerenga mawu a Yehova opatsidwa kwa mneneri Yeremiya, kuti Yerusalemu adzakhala bwinja kwa zaka 70.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 9:2
32 Mawu Ofanana  

kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, mpaka dziko linakondwera nao masabata ake; masiku onse a kupasuka kwake linasunga Sabata, kukwaniritsa zaka makumi asanu ndi awiri.


Chaka choyamba tsono cha Kirusi mfumu ya ku Persiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova m'kamwa mwa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Kirusi, kuti abukitse mau mu ufumu wake wonse, nawalembenso, ndi kuti,


Mboni zanu zomwe ndizo zondikondweretsa, ndizo zondipangira nzeru.


Mizinda yanu yopatulika yasanduka chipululu, Ziyoni wasanduka chipululu, Yerusalemu wasanduka bwinja.


Mau a Yeremiya mwana wa Hilikiya, wa ansembe amene anali ku Anatoti m'dziko la Benjamini;


Yerusalemu, ndi mizinda ya Yuda, ndi mafumu ake omwe, ndi akulu ake, kuwayesa iwo bwinja, chizizwitso, chotsonyetsa, ndi chitemberero; monga lero lino;


Mika Mmoreseti ananenera masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda; ndipo iye ananena kwa anthu onse a Yuda, kuti, Yehova wa makamu atero: Ziyoni adzalimidwa ngati munda, Yerusalemu adzakhala miunda, ndi phiri la nyumba longa misanje ya nkhalango.


pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mzinda uwu chitemberero cha kwa mitundu yonse ya dziko lapansi.


Ndipo amitundu onse adzamtumikira iye, ndi mwana wake, ndi mdzukulu wake, mpaka yafika nthawi ya dziko lake; ndipo amitundu ambiri ndi mafumu aakulu adzamuyesa iye mtumiki wao.


Pakuti Yehova atero, kuti, Zitapita zaka makumi asanu ndi awiri pa Babiloni, ndidzakuyang'anirani inu, ndipo ndidzakuchitirani inu mau anga abwino, ndi kubwezera inu kumalo kuno.


Ndipo ndidzaletsa m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, mau akukondwa ndi mau akusekera, ndi mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi; pakuti dziko lidzasanduka bwinja.


Ha! Mzindawo unadzala anthu, ukhalatu pa wokha! Ukunga mkazi wamasiye! Waukuluwo mwa amitundu, kalonga wamkazi m'madera a dziko wasanduka wolamba!


Silidzapitamo phazi la munthu, kapena phazi la nyama losapitamo, losakhalamo anthu zaka makumi anai.


Ndipo ndinaika nkhope yanga kwa Ambuye Mulungu, kumfunsa Iye m'pemphero, ndi mapembedzero, ndi kusala, ndi ziguduli, ndi mapulusa.


Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi mu Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango.


Ndipo mthenga wa Yehova anayankha nati, Yehova wa makamu, mudzakhala mpaka liti osachitira chifundo Yerusalemu, ndi mizinda ya Yuda, imene munakwiya nayo zaka izi makumi asanu ndi awiri?


Nena kwa anthu onse a m'dziko, ndi kwa ansembe, kuti, Muja mukasala ndi kulira mwezi wachisanu, ndi wachisanu ndi chitatu, zaka izi makumi asanu ndi awiri, kodi mukasalira Ine, Inedi?


Chifukwa chake m'mene mukadzaona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Daniele mneneri, chitaima m'malo oyera (iye amene awerenga m'kalata azindikire)


Ndipo pamene mukaona chonyansa cha kupululutsa chilikuima pomwe sichiyenera (wakuwerenga azindikire), pamenepo a mu Yudeya athawire kumapiri:


Ndipo mdindoyo anayankha Filipo, nati, Ndikupempha, mneneri anena ichi za yani? Za yekha, kapena za wina?


Kufikira ndidza ine, usamalire kuwerenga, kuchenjeza, kulangiza.


Wodala iye amene awerenga, ndi iwo amene akumva mau a chinenerocho, nasunga zolembedwa momwemo; pakuti nthawi yayandikira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa