Mtsinje wamoto unayenda wotuluka pamaso pake, zikwizikwi anamtumikira, ndi unyinji wosawerengeka unaima pamaso pake, woweruza mlandu anakhalapo, ndi mabuku anatsegulidwa.
Danieli 7:16 - Buku Lopatulika Ndinayandikira kwa wina wa iwo akuimako ndi kumfunsa za choonadi za ichi chonse. Ndipo ananena nane, nandidziwitsa kumasulira kwake kwa zinthuzi: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinayandikira kwa wina wa iwo akuimako ndi kumfunsa za choonadi za ichi chonse. Ndipo ananena nane, nandidziwitsa kumasulira kwake kwa zinthuzi: Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndinayandikira mmodzi mwa amene anayima pamenepo ndi kumufunsa tanthauzo lenileni la zonsezi. “Kotero anandiwuza ndi kundipatsa tanthauzo la zinthu zonse izi: |
Mtsinje wamoto unayenda wotuluka pamaso pake, zikwizikwi anamtumikira, ndi unyinji wosawerengeka unaima pamaso pake, woweruza mlandu anakhalapo, ndi mabuku anatsegulidwa.
Nayandikira iye poima inepo; atadza iye tsono ndinachita mantha, ndinagwa nkhope pansi; koma anati kwa ine, Zindikira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti masomphenyawo anena za nthawi ya chimaliziro.
Ndipo anandilangiza ine, ndi kulankhula nane, nati, Daniele iwe, ndatuluka tsopano ine kukuzindikiritsa mwaluntha.
Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Izi nziyani? Ndipo anandiyankha, Izi ndi nyangazi zinabalalitsa Yuda, Israele, ndi Yerusalemu.
Ndipo taonani, mthenga wolankhula nane anatuluka, ndi mthenga wina anatuluka kukomana naye,
Atero Yehova wa makamu: Ukadzayenda m'njira zanga, ndi kusunga udikiro wanga, pamenepo udzaweruza nyumba yanga, ndi kusunga mabwalo anga, ndipo ndidzakupatsa malo oyendamo mwa awa oimirirapo.
ndipo mmodzi wa akulu ananena ndi ine, Usalire: taona, Mkango wochokera m'fuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana kuti akhoza kutsegula buku ndi zizindikiro zake zisanu ndi ziwiri.