Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 7:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Ndinayandikira mmodzi mwa amene anayima pamenepo ndi kumufunsa tanthauzo lenileni la zonsezi. “Kotero anandiwuza ndi kundipatsa tanthauzo la zinthu zonse izi:

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

16 Ndinayandikira kwa wina wa iwo akuimako ndi kumfunsa za choonadi za ichi chonse. Ndipo ananena nane, nandidziwitsa kumasulira kwake kwa zinthuzi:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndinayandikira kwa wina wa iwo akuimako ndi kumfunsa za choonadi za ichi chonse. Ndipo ananena nane, nandidziwitsa kumasulira kwake kwa zinthuzi:

Onani mutuwo Koperani




Danieli 7:16
14 Mawu Ofanana  

Mtsinje wa moto unkayenda, kuchokera patsogolo pake. Anthu miyandamiyanda ankamutumikira; ndipo anthu osawerengeka anayima pamaso pake. Abwalo anakhala malo awo, ndipo mabuku anatsekulidwa.


‘Zirombo zikuluzikulu zinayi zija ndi maufumu anayi amene adzaoneka pa dziko lapansi.


Atayandikira kumene ndinayima, ndinachita mantha ndi kugwa chafufumimba. Iye anati, “Mwana wa munthu, zindikira kuti masomphenyawa akunena za nthawi yachimaliziro.”


Anandilangiza kuti, “Danieli ndabwera tsopano kuti ndikupatse nzeru kuti uzitha kumvetsa zinthu.


Ndinamufunsa mngelo amene amayankhula nane kuti, “Kodi zimenezi ndi chiyani?” Iye anandiyankha kuti, “Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, Israeli ndi Yerusalemu.”


Taonani, mngelo amene amayankhula nane uja akuchoka, mngelo wina anabwera kudzakumana naye


“Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ngati uyenda mʼnjira zanga ndi kusunga malamulo anga, pamenepo udzalamulira nyumba yanga ndi kuyangʼanira mabwalo anga, ndipo ndidzakulolani kuti mudzakhale pamodzi ndi amene ali panowa.


Tsono mmodzi mwa akuluakulu aja anati kwa ine, “Usalire! Taona, Mkango wa fuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana. Iye angathe kufutukula bukuli ndi kumatula zomatira zisanu ndi ziwirizo.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa