Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 1:19 - Buku Lopatulika

19 Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Izi nziyani? Ndipo anandiyankha, Izi ndi nyangazi zinabalalitsa Yuda, Israele, ndi Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Izi nziyani? Ndipo anandiyankha, Izi ndi nyangazi zinabalalitsa Yuda, Israele, ndi Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Ndidafunsa mngelo amene ankalankhula nane tanthauzo lake la nyanga zimenezo. Iye adandiyankha kuti, ‘Zimenezi ndizo mphamvu zapansi pano zimene zidabalalitsa anthu a ku Yuda, a ku Israele ndi a ku Yerusalemu.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Ndinamufunsa mngelo amene amayankhula nane kuti, “Kodi zimenezi ndi chiyani?” Iye anandiyankha kuti, “Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, Israeli ndi Yerusalemu.”

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 1:19
20 Mawu Ofanana  

Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zachitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi mudzagunda nazo Aaramu mpaka atatha psiti.


Atamva tsono adani a Yuda ndi Benjamini kuti ana aja a ndende analikumangira Yehova Mulungu wa Israele Kachisi,


Pamenepo anthu a m'dziko anafoketsa manja a anthu Ayuda, nawavuta pomanga,


Ndipo masiku a Arita-kisereksesi Bisilamu, Mitiredati, Tabeele, ndi anzao otsala, analembera kwa Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya; ndi chilembedwe chake cha kalatayo anamlemba mu Chiaramu, namsanduliza mu Chiaramu.


Nthawi yomweyi anawadzera Tatenai kazembe tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setari-Bozenai, ndi anzao, nanena nao motere, Anakulamulirani inu ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?


Ndinati kwa odzitamandira, musamachita zodzitamandira; ndi kwa oipa, Musamakweza nyanga;


musamakwezetsa nyanga yanu; musamalankhula ndi khosi louma.


Nyanga ya Mowabu yaduka, ndipo wathyoka mkono wake, ati Yehova.


Ndipo ndinamva munthuyo wovala bafuta wokhala pamwamba pamadzi a mumtsinje, nakweza dzanja lake lamanja ndi lamanzere kumwamba, nalumbira pali Iye wokhala ndi moyo kosatha, kuti zidzachitika nthawi, ndi nthawi zina, ndi nusu; ndipo atatha kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo zidzatha izi zonse.


Ndinayandikira kwa wina wa iwo akuimako ndi kumfunsa za choonadi za ichi chonse. Ndipo ananena nane, nandidziwitsa kumasulira kwake kwa zinthuzi:


inu okondwera nacho chopanda pake, ndi kuti, Kodi sitinadzilimbitse tokha ndi kulanda Karinaimu mwa mphamvu yathuyathu?


Munapyoza ndi maluti ake mutu wa ankhondo ake; anadza ngati kamvulumvulu kundimwaza; kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mobisika.


Ndipo ndinakweza maso anga, ndinapenya, taonani, nyanga zinai.


Pamenepo ndinati, Adzeranji awa? Ndipo ananena, nati, Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, wopandanso wina woweramutsa mutu wake; koma awa anadza kuziopsa, kugwetsa nyanga za amitundu, amene anakwezera dziko la Yuda nyanga zao kulimwaza.


Pamenepo ndinati, Awa ndi chinai, mbuyanga? Ndi mthenga wakulankhula ndi ine anati kwa ine, Ndidzakuonetsa awa ndi chiyani.


Ndipo ndinati, Upita kuti? Ndipo anati kwa ine, Kukayesa Yerusalemu, kuona ngati chitando chake nchotani, ndi m'litali mwake motani.


Pakuti atero Yehova wa makamu: Monga ndinalingirira kuchitira inu choipa, muja makolo anu anautsa mkwiyo wanga, ati Yehova wa makamu, ndipo sindinawaleke;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa