Ndipo kuyamba kwake kwa ufumu wake kunali Babiloni, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m'dziko la Sinara.
Danieli 4:30 - Buku Lopatulika Mfumu inanena, niti, Suyu Babiloni wamkulu ndinammanga, akhale pokhala pachifumu, ndi mphamvu yanga yaikulu uoneke ulemerero wachifumu wanga? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mfumu inanena, niti, Suyu Babiloni wamkulu ndinammanga, akhale pokhala pachifumu, ndi mphamvu yanga yaikulu uoneke ulemerero wa chifumu changa? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero iye anati, “Kodi Babuloni si mzinda wamphamvu ndi wokongola umene ndinamanga ndi mphamvu zanga ngati nyumba yanga yaufumu, kuonetsera ulemerero wa ufumu wanga?” |
Ndipo kuyamba kwake kwa ufumu wake kunali Babiloni, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m'dziko la Sinara.
pamene anaonetsa zolemera za ufumu wake waulemu, ndi ulemerero wa ukulu wake woposa, masiku ambiri, ndiwo masiku zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu.
Kudzikuza kwa munthu kudzamchepetsa; koma wokhala ndi mtima wodzichepetsa adzalemekezedwa.
Ndipo Babiloni, ulemerero wa maufumu, mudzi wokongolawo Ababiloni anaunyadira, adzakhala monga momwe Mulungu anapasula Sodomu ndi Gomora.
nena, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona nditsutsana nawe, Farao mfumu ya Aejipito, ng'ona yaikulu yakugona m'kati mwa mitsinje yake, imene ikuti, Mtsinje wanga ndi wangatu, ndadzipangira ndekha uwu.
Akali m'kamwa mwa mfumu mau awa, anamgwera mau ochokera kumwamba, ndi kuti, Mfumu Nebukadinezara, anena kwa iwe: ufumu wakuchokera.
Pamenepo adzapitirira ngati mphepo, nadzalakwa ndi kupalamula, iye amene aiyesa mphamvu yake mulungu wake.
Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.
ndipo pakufika iye amene adaitana iwe ndi uyu, adzati kwa iwe, Mpatse uyu malo; ndipo pomwepo udzayamba manyazi kukhala pa mpando wa kuthungo.
Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.
Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.
Ndipo anatsata mngelo wina mnzake ndi kunena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu umene unamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake.
Ndipo chimzinda chachikulucho chidagawika patatu, ndi mizinda ya amitundu inagwa; ndipo Babiloni waukulu unakumbukika pamaso pa Mulungu, kuti aupatse chikho cha vinyo waukali wa mkwiyo wake.
ndipo pamphumi pake padalembedwa dzina, CHINSINSI, BABILONI WAUKULU, AMAI WA ACHIGOLOLO NDI WA ZONYANSITSA ZA DZIKO.
chifukwa chakuopa chizunzo chake, nanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukuluwo, Babiloni, mzinda wolimba! Pakuti mu ora limodzi chafika chiweruziro chanu.
Ndipo mngelo wolimba ananyamula mwala ngati mphero yaikulu, naiponya m'nyanja, nanena, Chotero Babiloni, mzinda waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse.