Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 3:13 - Buku Lopatulika

Pamenepo Nebukadinezara, mumkwiyo ndi mu ukali wake, anawauza abwere nao Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego. Ndipo anabwera nao amunawa kwa mfumu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pamenepo Nebukadinezara, mumkwiyo ndi m'ukali wake, anawauza abwere nao Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego. Ndipo anabwera nao amunawa kwa mfumu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tsono Nebukadinezara anakwiya ndi kupsa mtima kwambiri, ndipo anayitanitsa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego. Choncho amuna awa anabwera pamaso pa mfumu,

Onani mutuwo



Danieli 3:13
15 Mawu Ofanana  

koma sanayang'anire Kaini ndi nsembe yake. Kaini ndipo anakwiya kwambiri, ndipo nkhope yake inagwa.


Kukomana ndi chitsiru m'kupusa kwake kuopsa koposa chilombo chochichotsera anake.


Mwala ulemera, mchenga ndiwo katundu; koma mkwiyo wa chitsiru upambana kulemera kwake.


Mwamuna wamkwiyo aputa makangano; waukali achuluka zolakwa.


Ndi mkulu wa adindo anawapatsa maina ena; Daniele anamutcha Belitesazara; ndi Hananiya, Sadrake; ndi Misaele, Mesaki; ndi Azariya, Abedenego.


Chifukwa chake mfumu inakwiya, nizaza kwambiri, nilamulira kuti awaphe anzeru onse mu Babiloni.


Pamenepo Nebukadinezara anadzazidwa ndi ukali, ndi maonekedwe a nkhope yake anasandulikira Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego; anayankha, nati asonkheze ng'anjo kasanu ndi kawiri koposa umo amasonkhezera.


ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja.


Koma inu mudziyang'anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu ku bwalo la akulu a milandu; ndipo adzakukwapulani m'masunagoge; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafumu mudzaimirira chifukwa cha Ine, kukhale umboni kwa iwo.


Koma zisanachitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, chifukwa cha dzina langa.


Koma iwowo anagwidwa misala; nalankhulana wina ndi mnzake kuti amchitire Yesu chiyani.


Koma atapita masiku ena, anadza Felikisi ndi Durusila mkazi wake, ndiye Myuda, naitana Paulo, ndipo anamva iye za chikhulupiriro cha Khristu Yesu.