Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 21:12 - Buku Lopatulika

12 Koma zisanachitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, chifukwa cha dzina langa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Koma zisanachitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, chifukwa cha dzina langa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 “Koma zisanachitike zonsezi, adzakugwirani ndi kukuzunzani. Adzapita nanu ku milandu ku nyumba zamapemphero, nadzakuponyani m'ndende. Adzakuperekani kwa mafumu ndi kwa akulu ena a Boma chifukwa chotsatira Ine.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 “Koma zonsezi zisanachitike, adzakugwirani ndi kukuzunzani. Adzakuperekani ku masunagoge ndi ku ndende, ndipo adzakutengerani pamaso pa mafumu ndi olamulira, ndipo zonsezi zidzachitika chifukwa cha dzina langa.

Onani mutuwo Koperani




Luka 21:12
31 Mawu Ofanana  

ndipo otsala anagwira akapolo ake, nawachitira chipongwe, nawapha.


Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba.


ndipo kudzakhala zivomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri m'malo akutiakuti, ndipo kudzakhala zoopsa ndi zizindikiro zazikulu zakumwamba.


Kumbukirani mau amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulondalondani inunso; ngati anasunga mau anga, adzasunga anunso.


Koma izi zonse adzakuchitirani chifukwa cha dzina langa, chifukwa sadziwa wondituma Ine.


Koma m'mawa mwake pofuna kuzindikira chifukwa chake chenicheni chakuti anamnenera Ayuda, anammasula iye, nalamulira asonkhane ansembe aakulu, ndi bwalo lonse la akulu a milandu, ndipo anatsika naye Paulo, namuika pamaso pao.


Ndipo anavomerezana ndi iye; ndipo m'mene adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.


Ndipo Saulo anapasula Mpingo, nalowa nyumba ndi nyumba, nakokamo amuna ndi akazi, nawaika m'ndende.


ndipo anagwa pansi, namva mau akunena naye, Saulo, Saulo, Undilondalonderanji?


Tadzigonjani kwa zoikika zonse za anthu, chifukwa cha Ambuye; ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse;


Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa