Marko 13:9 - Buku Lopatulika9 Koma inu mudziyang'anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu ku bwalo la akulu a milandu; ndipo adzakukwapulani m'masunagoge; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafumu mudzaimirira chifukwa cha Ine, kukhale umboni kwa iwo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Koma inu mudziyang'anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a milandu; ndipo adzakukwapulani m'masunagoge; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafumu mudzaimirira chifukwa cha Ine, kukhale umboni kwa iwo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 “Koma inu muchenjere. Anthu adzakuperekani ku mabwalo amilandu a Ayuda, ndipo adzakukwapulani m'nyumba zao zamapemphero. Mudzaonekera kwa akulu a Boma ndi kwa mafumu chifukwa cha Ine, kuti mukandichitire umboni pamaso pao. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 “Muyenera kukhala tcheru. Mudzaperekedwa ku mabwalo oweruza ndi kukwapulidwa mwankhanza mʼmasunagoge. Mudzayima pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu monga mboni kwa iwo chifukwa cha Ine. Onani mutuwo |