Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 3:19 - Buku Lopatulika

19 Pamenepo Nebukadinezara anadzazidwa ndi ukali, ndi maonekedwe a nkhope yake anasandulikira Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego; anayankha, nati asonkheze ng'anjo kasanu ndi kawiri koposa umo amasonkhezera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Pamenepo Nebukadinezara anadzazidwa ndi ukali, ndi maonekedwe a nkhope yake anansandulikira Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego; anayankha, nati asonkheze ng'anjo kasanu ndi kawiri koposa umo amasonkhezera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Pamenepo Nebukadinezara anapsa mtima ndi Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, ndipo anayipidwa nawo. Iye analamulira kuti ngʼanjo ayitenthetse kasanu ndi kawiri kuposa nthawi zonse,

Onani mutuwo Koperani




Danieli 3:19
26 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anaona nkhope ya Labani, taonani, siinamuonekere iye monga kale.


Ndipo Hamani, pakuona kuti Mordekai sanamweramire kapena kumgwadira, mtima wake unadzala mkwiyo.


Ninyamuka mfumu mu mkwiyo wake ku madyerero a vinyo, nimka kumunda wa maluwa wa kuchinyumba; koma Hamani anatsalira kudzipempherera moyo kwa mkazi wamkulu Estere; popeza anapenya kuti mfumu inatsimikiza mtima kumchitira choipa.


Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani; chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.


Mkwiyo wa mfumu ndi mithenga ya imfa; wanzeru adzaukhulula.


Wonyada wodzikuza dzina lake ndiye wonyoza; achita mwaukali modzitama.


Ndidzachiika m'dzanja la iwo amene avutitsa iwe; amene anena kumoyo wako, Gwada pansi kuti ife tipite; ndipo iwe wagonetsa pamsana pako monga pansi, ndi monga khwalala kwa iwo amene apita pamenepo.


Chifukwa chake mfumu inakwiya, nizaza kwambiri, nilamulira kuti awaphe anzeru onse mu Babiloni.


Pamenepo Nebukadinezara, mumkwiyo ndi mu ukali wake, anawauza abwere nao Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego. Ndipo anabwera nao amunawa kwa mfumu.


Nauza amuna ena amphamvu a m'khamu lake la nkhondo amange Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, ndi kuwaponya m'ng'anjo yotentha yamoto.


Pamenepo padasandulika pa nkhope pake pa mfumu, ndi maganizo ake anamsautsa, ndi mfundo za m'chuuno mwake zinaguluka, ndi maondo ake anaombana.


Ndipo italamulira mfumu, anabwera nao amuna aja adamneneza Daniele, nawaponya m'dzenje la mikango, iwowa, ana ao, ndi akazi ao; ndipo asanafike pansi pa dzenje mikango inawaposa mphamvu, niphwanya mafupa ao onse.


Ndipo mukapanda kundimvera, zingakhale izi, ndidzaonjeza kukulangani kasanu ndi kawiri chifukwa cha zochimwa zanu.


Ndipo mukayenda motsutsana nane, osalola kumvera Ine; ndidzakuonjezerani miliri kasanu ndi kawiri, monga mwa zochimwa zanu.


Inenso ndidzayenda motsutsana ndi inu; ndipo ndidzakukanthani Inedi kasanu ndi kawiri chifukwa cha zoipa zanu.


Ine ndidzayenda nanu motsutsana mwa kukuzazirani, ndi kukulangani Inedi kasanu ndi kawiri chifukwa cha zochimwa zanu.


Koma m'mene anamva iwo analaswa mtima, nafuna kuwapha.


Koma pakumva izi analaswa mtima, namkukutira mano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa