Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 3:19 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Pamenepo Nebukadinezara anapsa mtima ndi Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, ndipo anayipidwa nawo. Iye analamulira kuti ngʼanjo ayitenthetse kasanu ndi kawiri kuposa nthawi zonse,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

19 Pamenepo Nebukadinezara anadzazidwa ndi ukali, ndi maonekedwe a nkhope yake anasandulikira Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego; anayankha, nati asonkheze ng'anjo kasanu ndi kawiri koposa umo amasonkhezera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Pamenepo Nebukadinezara anadzazidwa ndi ukali, ndi maonekedwe a nkhope yake anansandulikira Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego; anayankha, nati asonkheze ng'anjo kasanu ndi kawiri koposa umo amasonkhezera.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 3:19
26 Mawu Ofanana  

Choncho Yakobo anaona kuti Labani sankamuonetsanso nkhope yabwino monga kale.


Hamani ataona kuti Mordekai sankamugwadira kapena kumuweramira, anapsa mtima kwambiri.


Mfumu itakwiya kwambiri inanyamuka pa phwando nipita ku munda wa maluwa wa nyumba yaufumu. Koma Hamani, pozindikira kuti mfumu yaganiza kale kumuchitira choyipa, anatsalira mʼnyumba kupempha Estere kuti apulumutse moyo wake.


Zoonadi, ukali wanu pa anthu umakubweretserani matamando ndipo opulumuka ku ukali wanu mumawasunga pafupi nanu.


Ukali wa mfumu ndi mthenga wa imfa, koma munthu wanzeru amawupepesa ukaliwo.


Munthu wonyada ndi wodzikuza amamutcha, “Mnyodoli,” iye amachita zinthu modzitama kwambiri.


Ndidzapereka chikhocho kwa anthu amene amakuzunza, amene ankakuwuza kuti, ‘gona pansi tikuyende pa msana.’ Ndipo msana wako anawuyesa pansi popondapo, ngati msewu woti ayendepo.”


Zimenezi zinapsetsa mtima mfumu ndipo inakwiya kwambiri kotero inalamula kuti anzeru onse a ku Babuloni aphedwe.


Tsono Nebukadinezara anakwiya ndi kupsa mtima kwambiri, ndipo anayitanitsa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego. Choncho amuna awa anabwera pamaso pa mfumu,


ndipo analamula ena mwa asilikali amphamvu kwambiri mʼgulu lake lankhondo kuti amange Sadirake, Mesaki ndi Abedenego ndi kuwaponya mʼngʼanjo ya moto.


Nkhope yake inasandulika ndipo inachita mantha, nkhongono zii, mawondo gwedegwede.


Mwa lamulo la mfumu, anthu onse amene ananeneza Danieli aja anagwidwa ndi kukaponyedwa mʼdzenje la mikango, pamodzi ndi akazi awo ndi ana awo. Ndipo asanafike pansi pa dzenjelo, mikango inawawakha ndi mphamvu ndi kuteketa mafupa awo onse.


“ ‘Ngati simudzandimvera mutaona zonsezi, ndidzakulanganinso mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha kuchimwa kwanu.


“ ‘Ngati mudzapitirira kutsutsana nane ndi kukana kundimvera, ndidzachulukitsa masautso anu kasanu ndi kawiri molingana ndi machimo anu.


Ine mwini ndidzalimbana nanu, ndipo ndidzakulangani mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha machimo anu.


pamenepo ndidzalimbana nanu mwaukali, ndipo Ine mwini ndidzakulangani mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha kuchimwa kwanu.


Akuluakuluwo atamva zimenezi anakwiya kwambiri nafuna kuwapha.


Atamva zimenezi, iwo anakwiya kwambiri ndipo anamukukutira mano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa