Potero mfumu inakhala upo, napanga anaang'ombe awiri agolide, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisraele inu milungu yanu, imene inakutulutsani m'dziko la Ejipito.
Danieli 3:1 - Buku Lopatulika Mfumu Nebukadinezara anapanga fano lagolide, msinkhu wake mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi thunthu lake mikono isanu ndi umodzi; analiimika pa chidikha cha Dura, m'dera la ku Babiloni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mfumu Nebukadinezara anapanga fano lagolide, msinkhu wake mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi thunthu lake mikono isanu ndi umodzi; analiimika pa chidikha cha Dura, m'dera la ku Babiloni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumu Nebukadinezara anapangitsa fano la golide lotalika mamita 27 ndi mulifupi mwake mamita atatu, ndipo analiyimika mʼchigwa cha Dura mʼchigawo cha Babuloni. |
Potero mfumu inakhala upo, napanga anaang'ombe awiri agolide, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisraele inu milungu yanu, imene inakutulutsani m'dziko la Ejipito.
Izi zinachitika masiku a Ahasuwero, ndiye Ahasuweroyo anachita ufumu kuyambira Indiya kufikira Kusi, pa maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri.
Ndipo Mose anabwerera kunka kwa Yehova, nati, Ha! Pepani, anthu awa anachimwa kuchimwa kwakukulu, nadzipangira milungu yagolide.
Tsiku limenelo munthu adzataya kumfuko ndi kumileme mafano ake asiliva ndi agolide amene anthu anampangira iye awapembedze;
Ndipo mudzaipitsa chokuta cha mafano ako, osema asiliva, ndi chomata cha mafano ako osungunula agolide; udzawataya ngati kanthu konyansa, udzati kwa iwo, Chokani.
Amene ataya golide, namtulutsa m'thumba, ndi kuyesa siliva ndi muyeso, iwo alemba wosula golide; iye napanga nazo mulungu; iwo agwada pansi, inde alambira.
Abwera ndi siliva wa ku Tarisisi, wosulasula wopyapyala ndi golide wa ku Ufazi, ntchito ya mmisiri ndi manja a woyenga; zovala zao ndi nsalu ya madzi ndi yofiirira; zonsezi ndi ntchito za muomba.
Pamenepo mfumu inasandutsa Daniele wamkulu, nimpatsa mphatso zazikulu zambiri, namlamuliritsa dera lonse la ku Babiloni; nakhala iye kazembe wamkulu wa anzeru onse a ku Babiloni.
Pamenepo Daniele anapempha mfumu, ndipo anaika Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, ayang'anire ntchito za dera la ku Babiloni. Koma Daniele anakhala m'bwalo la mfumu.
Nebukadinezara anayankha, nati kwa iwo, Kodi mutero dala, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, kusatumikira milungu yanga, ndi kusalambira fano lagolide ndinaliimikalo?
koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu aang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitire ulemu.
Anamwa vinyo, nalemekeza milungu yagolide, ndi yasiliva, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala.
Pakuti sanadziwe kuti ndine ndinampatsa tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi kumchulukitsira siliva ndi golide, zimene anapanga nazo Baala.
Analonga mafumu, koma sikunachokera kwa Ine; anaika akalonga, koma sindinadziwa; anadzipangira mafano a siliva wao ndi golide wao, kuti akalikhidwe.
Tsoka iye wakunena kwa mtengo, Galamuka; ndi kwa mwala wosalankhula, Nyamuka! Kodi ichi chiphunzitsa? Taona chakutidwa ndi golide ndi siliva, ndi m'kati mwake mulibe mpweya konse.
Popeza tsono tili mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanafana ndi golide, kapena siliva, kapena mwala, wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu.
Ndipo muona ndi kumva, kuti si pa Efeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, Paulo uyu akopa ndi kutembenutsa anthu ambiri, ndi kuti, Si milungu iyi imene ipangidwa ndi manja:
Mafano osema a milungu yao muwatenthe ndi moto; musamasirira siliva ndi golide zili pa iwo, kapena kudzitengera izi; mungakodwe nazo; pakuti izi zinyansira Yehova Mulungu wanu.
Ndipo otsala a anthu osaphedwa nayo miliri iyo sanalape ntchito ya manja ao, kuti asapembedzere ziwanda, ndi mafano agolide, ndi asiliva, ndi amkuwa, ndi a mwala, ndi amtengo, amene sangathe kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda;