Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 17:29 - Buku Lopatulika

29 Popeza tsono tili mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanafana ndi golide, kapena siliva, kapena mwala, wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Popeza tsono tili mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanafana ndi golide, kapena siliva, kapena mwala, wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 “Tsono popeza kuti tili ngati ana a Mulungu, sitiyenera kuganiza kuti umulungu wake umafanafana ndi fano lagolide kapena lasiliva kapena lamwala, lopangidwa mwa luso ndi nzeru za munthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 “Tsono popeza ndife ana a Mulungu, tisaganize kuti umulungu wake ndi wofanana ndi ndalama zagolide, zasiliva, mwala, kapenanso fanizo lopangidwa mwaluso la nzeru za anthu.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 17:29
14 Mawu Ofanana  

naponya milungu yao kumoto; popeza sindiyo milungu koma yopanga anthu ndi manja ao, mtengo ndi mwala; chifukwa chake anaiononga.


M'mwemo anasintha ulemerero wao ndi fanizo la ng'ombe yakudya msipu.


Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi padziko.


Ndipo anazilandira ku manja ao, nachikonza ndi chozokotera, nachiyenga mwanawang'ombe; ndipo anati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m'dziko la Ejipito.


Mudzandifanizira Ine ndi yani tsono, kuti ndilingane naye, ati Woyerayo.


Ndipo muona ndi kumva, kuti si pa Efeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, Paulo uyu akopa ndi kutembenutsa anthu ambiri, ndi kuti, Si milungu iyi imene ipangidwa ndi manja:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa