Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 10:9 - Buku Lopatulika

9 Abwera ndi siliva wa ku Tarisisi, wosulasula wopyapyala ndi golide wa ku Ufazi, ntchito ya mmisiri ndi manja a woyenga; zovala zao ndi nsalu ya madzi ndi yofiirira; zonsezi ndi ntchito za muomba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Abwera ndi siliva wa ku Tarisisi, wosulasula wopyapyala ndi golide wa ku Ufazi, ntchito ya mmisiri ndi manja a woyenga; zovala zao ndi nsalu ya madzi ndi yofiirira; zonsezi ndi ntchito za muomba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Siliva wosula wokutira mafanowo ndi wochokera ku Tarisisi, ndipo golide wake ndi wochokera ku Ufazi. Mafano aowo ndi ntchito ya anthu aluso ndi anthu odziŵa kuzokota golide. Amaveka mafanowo nsalu zonyezimira ndi zofiirira. Zonsezo ndi ntchito ya anthu aluso chabe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Siliva wosula amabwera naye kuchokera ku Tarisisi ndipo golide amachokera naye ku Ufazi. Mafanowo ndi ntchito ya anthu aluso ndi odziwa kuzokota golide. Tsono mafanowo amawaveka zovala za mtundu wamtambo ndi pepo. Yonseyo ndi ntchito ya anthu a luso.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 10:9
12 Mawu Ofanana  

Popeza mfumu inali nazo panyanja zombo za ku Tarisisi, pamodzi ndi zombo za Hiramu; zombo za ku Tarisisi zinafika kamodzi zitapita zaka zitatu, zili nazo golide, ndi siliva, ndi minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za mawangamawanga.


Pakuti zombo za mfumu zinayenda ku Tarisisi ndi anyamata a Huramu; zombo za ku Tarisisi zinadza kamodzi zitapita zaka zitatu, ndi kubwera nazo golide, ndi siliva, minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za mawangamawanga.


Mafano ao ndiwo a siliva ndi golide, ntchito za manja a anthu.


Mafumu a ku Tarisisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera nacho chopereka; mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso.


Olokani inu, kunka ku Tarisisi, kuwani, inu okhala m'chisumbu.


Fano losema mmisiri analisungunula, ndipo wosula golide analikuta ndi golide, naliyengera maunyolo asiliva.


Tarisisi anagulana nawe malonda m'kuchuluka kwa chuma chilichonse; anagula malonda ako ndi siliva ndi chitsulo, seta ndi ntovu.


Thanga lako ndi labafuta wopikapika wa ku Ejipito, likhale ngati mbendera yako; chophimba chako ndicho nsalu yamadzi ndi yofiirira zochokera ku zisumbu za Elisa.


ndinakweza maso anga, ndinapenya ndi kuona munthu wovala bafuta, womanga m'chuuno ndi golide woona wa ku Ufazi;


Pakuti ichi chomwe chafumira kwa Israele; mmisiri wampanga, koma sali Mulungu; inde mwanawang'ombe wa Samariya adzaphwanyikaphwanyika.


Koma Yona ananyamuka kuti athawire ku Tarisisi, kuzemba Yehova; ndipo anatsikira ku Yopa, napezako chombo chomuka ku Tarisisi, napereka ndalama zake, natsikira m'menemo, kuti apite nao ku Tarisisi kuzemba Yehova.


Tsoka iye wakunena kwa mtengo, Galamuka; ndi kwa mwala wosalankhula, Nyamuka! Kodi ichi chiphunzitsa? Taona chakutidwa ndi golide ndi siliva, ndi m'kati mwake mulibe mpweya konse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa