Hoseya 2:8 - Buku Lopatulika8 Pakuti sanadziwe kuti ndine ndinampatsa tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi kumchulukitsira siliva ndi golide, zimene anapanga nazo Baala. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Pakuti sanadziwa kuti ndine ndinampatsa tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi kumchulukitsira siliva ndi golide, zimene anapanga nazo Baala. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Sankadziŵa kuti ndine amene ndinkamupatsa tirigu, vinyo ndi mafuta. Sankadziŵa kuti ndine amene ndinkamupatsa siliva ndi golide wambiri zimene anthuwo ankapangira mafano a Baala. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Iye sanazindikire kuti ndine amene ndinkamupatsa tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta. Ndine amene ndinkamukhuthulira siliva ndi golide, zimene ankapangira mafano a Baala. Onani mutuwo |
koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu aang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitire ulemu.