Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 2:9 - Buku Lopatulika

9 Chifukwa chake ndidzabwera ndi kuchotsa tirigu wanga m'nyengo yake, ndi vinyo wanga m'nthawi yake yoikika, ndi kukwatula ubweya wanga ndi thonje langa, zimene zikadafunda umaliseche wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Chifukwa chake ndidzabwera ndi kuchotsa tirigu wanga m'nyengo yake, ndi vinyo wanga m'nthawi yake yoikika, ndi kukwatula ubweya wanga ndi thonje langa, zimene zikadafunda umaliseche wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Nchifukwa chake ndidzamlanda tirigu wanga pa nthaŵi yodula ndi vinyo wanga pa nthaŵi yofinya. Ndidzamlandanso ubweya ndi thonje langa zimene ankavalira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “Choncho Ine ndidzamulanda tirigu wanga pa nthawi yokolola, ndi vinyo wanga watsopano pa nthawi yopsinya mphesa. Ndidzamulanda ubweya ndi thonje langa, zomwe akanaphimba nazo umaliseche wake.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 2:9
15 Mawu Ofanana  

Taona tsono, ndakutambasulira dzanja langa, ndi kuchepsa gawo lako la chakudya, ndi kukupereka ku chifuniro cha iwo akudana nawe, kwa ana aakazi a Afilisti akuchita manyazi ndi njira yako yoipa.


Ndidzakuperekanso m'dzanja lao, ndipo adzagwetsa nyumba yako yachimphuli, ndi kugumula ziunda zako, nadzakuvula zovala zako, ndi kulanda zokometsera zako zokongola, nadzakusiya wamaliseche ndi wausiwa.


Adzakuvulanso zovala zako, ndi kukuchotsera zokometsera zako zokongola.


Ndi mfumu ya kumpoto idzabwera, nidzaimika unyinji wakuposa oyamba aja; nidzafika pachimaliziro cha nthawi, cha zaka, ndi khamu lalikulu la nkhondo ndi chuma chambiri.


ndingamvule wamaliseche, ndi kumuika ngati tsiku lija anabadwalo, ndi kumsanduliza ngati chipululu, ndi kumuika ngati dziko louma, ndi kumupha nalo ludzu;


Pakuti abzala mphepo, nadzakolola kamvulumvulu; alibe tirigu wosasenga; ngala siidzatulutsa ufa; chinkana iutulutsa, alendo adzaumeza.


Dwale ndi choponderamo mphesa sizidzawadyetsa, vinyo watsopano adzamsowa.


Kaya, kapena adzabwerera, nadzalekerera, ndi kusiya mdalitso pambuyo pake, ndiwo nsembe yaufa ndi nsembe yothira ya Yehova Mulungu wanu.


Ndipo zolemera zao zidzakhala zakufunkhidwa; ndi nyumba zao zabwinja; adzamangadi nyumba, koma sadzagonamo; adzaoka minda yampesa koma sadzamwa vinyo wake.


Chinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawatcha, Dziko la choipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao chikwiyire.


Pamenepo mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa