Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 2:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo tsopano ndidzaonetsa manyazi ake pamaso pa omkonda, popandanso wakumlanditsa m'dzanja langa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo tsopano ndidzaonetsa manyazi ake pamaso pa omkonda, popandanso wakumlanditsa m'dzanja langa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Motero ndidzaonetsa dama lake poyera kwa zibwenzi zake, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzampulumutse m'manja mwanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Motero tsopano ndidzaonetsa maliseche ake pamaso pa zibwenzi zake; palibe ndi mmodzi yemwe adzamupulumutse mʼmanja mwanga.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 2:10
19 Mawu Ofanana  

Pakuti ana a Ataliya mkazi woipa uja anathyola chitseko cha nyumba ya Mulungu, natenga zopatulidwa zonse za nyumba ya Yehova kuzipereka kwa Baala.


Dziwitsani ichi inu oiwala Mulungu, kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi.


Zoonadi, wochimwa sadzapulumuka chilango; koma mbeu ya olungama idzalanditsidwa.


chifukwa chake Ambuye adzachita nkanambo pa liwombo la ana aakazi a Ziyoni, ndipo Yehova adzavundukula m'chuuno mwao.


Ndipo ngati udzati m'mtima mwako, Zimenezi zandifikira ine chifukwa ninji? Chifukwa cha choipa chako chachikulu nsalu zako zoyesa mfula zasanduka mbudulira, ndi zitendene zako zaphwetekwa.


Chifukwa chake Ine ndidzaonetsa zotopola mikawo zako, pamaso pako, ndipo manyazi ako adzaoneka.


Ndipo unatengako zovala zako, ndi kudzimangira misanje ya mawangamawanga, ndi kuchitapo chigololo; zotere sizinayenere kufika kapena kuchitika.


Ndi mkate wanga ndinakupatsawo, ufa wosalala, ndi mafuta, ndi uchi, ndinakudyetsazo, unawaikira izi pamaso pao, zichite fungo lokoma; kunatero, ati Ambuye Yehova.


ndipo adzachita nawe mwaudani, nadzalanda zonse udazigwirira ntchito, nadzakusiya wamaliseche ndi wausiwa; ndi umaliseche wa zigololo zako udzavulidwa, dama lako ndi zigololo zako zomwe.


Israele ndi mpesa wotambalala, wodzibalira wokha zipatso; monga umo zinachulukira zipatso zake, momwemo anachulukitsa maguwa a nsembe ake; monga mwa kukoma kwake kwa dziko lake anapanga zoimiritsa zokoma.


Pamene Efuremu analankhula panali kunjenjemera; anadzikweza mu Israele; koma pamene anapalamula mwa Baala, anafa.


ndingamvule wamaliseche, ndi kumuika ngati tsiku lija anabadwalo, ndi kumsanduliza ngati chipululu, ndi kumuika ngati dziko louma, ndi kumupha nalo ludzu;


Ndipo monga magulu a mbala alalira munthu, momwemo msonkhano wa ansembe amapha panjira ya ku Sekemu; indedi achita choipitsitsa.


Ndipo otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama zakuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.


Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa