Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.
Danieli 1:9 - Buku Lopatulika Ndipo Mulungu anamkometsera Daniele mtima wa mkulu wa adindo, amchitire chifundo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mulungu anamkometsera Daniele mtima wa mkulu wa adindo, amchitire chifundo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Mulungu anafewetsa mtima wa ndunayo kuti amukomere mtima ndi kumuchitira chifundo Danieli, |
Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.
Koma Yehova anali ndi Yosefe namchitira iye zokoma, nampatsa ufulu pamaso pa woyang'anira kaidi.
ndi kukhululukira anthu anu adachimwira Inu ndi mphulupulu zao zonse adapalamula nazo kwa Inu; ndipo muwachititsire chifundo iwo amene anawagwira ndende, kuti awachitire chifundo;
Ambuye, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake.
Ndipo namwaliyo anamkomera, namchitira chifundo; ndipo anafulumira kumpatsa zake zomyeretsa, ndi magawo ake, ndi anamwali asanu ndi awiri oyenera kumpatsa ochokera m'nyumba ya mfumu; ndipo anamsuntha iye ndi anamwali ake akhale m'malo okometsetsa m'nyumba ya akazi.
Koma dziwani kuti Yehova anadzipatulira yekha womkondayo, adzamva Yehova m'mene ndimfuulira Iye.
Nati mkulu wa adindo kwa Daniele, Ine ndiopa mbuyanga mfumu, amene anakuikirani chakudya chanu ndi chakumwa chanu; pakuti aonerenji nkhope zanu zachisoni zoposa za anyamata olingana ndi inu? Momwemo mudzapalamulitsa mutu wanga kwa mfumu.
namlanditsa iye m'zisautso zake zonse, nampatsa chisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Ejipito; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Ejipito ndi pa nyumba yake yonse.