Danieli 1:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Ndipo Mulungu anafewetsa mtima wa ndunayo kuti amukomere mtima ndi kumuchitira chifundo Danieli, Onani mutuwoBuku Lopatulika9 Ndipo Mulungu anamkometsera Daniele mtima wa mkulu wa adindo, amchitire chifundo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ndipo Mulungu anamkometsera Daniele mtima wa mkulu wa adindo, amchitire chifundo. Onani mutuwo |
Inu Ambuye tcherani khutu lanu kuti mumve pemphero la mtumiki wanune ndiponso pemphero la atumiki anu amene amakondwera kuchitira ulemu dzina lanu. Lolani kuti mtumiki wanune zinthu zindiyendere bwino lero ndi kuti mfumu indichitire chifundo.” Nthawi imeneyi nʼkuti ndili woperekera zakumwa kwa mfumu.
Hegai anasangalatsidwa naye namwaliyo ndipo anamukomera mtima. Mosataya nthawi anamupatsa mafuta ake odzola ndi chakudya chapadera. Anamusankhiranso anamwali asanu ndi awiri a ku nyumba ya mfumu kuti azimutumikira, ndipo iye pamodzi ndi anamwali omutumikira aja anawapatsa malo abwino koposa mʼnyumba yosungira akazi.