Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Afilipi 4:14 - Buku Lopatulika

Koma munachita bwino kuti munayanjana nane m'chisautso changa.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma munachita bwino kuti munayanjana nane m'chisautso changa.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Komabe mudaachita bwino kundithandiza pa zovuta zanga.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Komatu munachita bwino kundithandiza mʼmavuto anga.

Onani mutuwo



Afilipi 4:14
14 Mawu Ofanana  

Koma Yehova ananena ndi Davide atate wanga, Popeza unafuna m'mtima mwako kumangira dzina langa nyumba, unachita bwino kuti m'mtima mwako unatero.


Koma Yehova anati kwa Davide atate wanga, Popeza unafuna mumtima mwako kulimangira dzina langa nyumba, unachita bwino kuti unatero mumtima mwako;


Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako.


Pakuti kunakondweretsa iwo; ndiponso iwo ali amangawa ao. Pakuti ngati amitundu anagawana zinthu zao zauzimu, alinso amangawa akutumikira iwo ndi zinthu zathupi.


Koma iye amene aphunzira mau, ayenera kuchereza womphunzitsayo m'zonse zabwino.


monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndili nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'chisomo.


Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.


kuti achite zabwino, nachuluke ndi ntchito zabwino, nakondwere kugawira ena, nayanjane;


pena pochitidwa chinthu chooneredwa mwa matonzo ndi zisautso; penanso polawana nao iwo ochitidwa zotere.


Pakuti munamva chifundo ndi iwo a m'ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa chuma chanu, pozindikira kuti muli nacho nokha chuma choposa chachikhalire.


Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.


Ine Yohane, mbale wanu ndi woyanjana nanu m'chisautso ndi ufumu ndi chipiriro zokhala mwa Yesu, ndinakhala pa chisumbu chotchedwa Patimosi, chifukwa cha mau a Mulungu ndi umboni wa Yesu.