Chivumbulutso 1:9 - Buku Lopatulika9 Ine Yohane, mbale wanu ndi woyanjana nanu m'chisautso ndi ufumu ndi chipiriro zokhala mwa Yesu, ndinakhala pa chisumbu chotchedwa Patimosi, chifukwa cha mau a Mulungu ndi umboni wa Yesu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ine Yohane, mbale wanu ndi woyanjana nanu m'chisautso ndi ufumu ndi chipiriro zokhala mwa Yesu, ndinakhala pa chisumbu chotchedwa Patimosi, chifukwa cha mau a Mulungu ndi umboni wa Yesu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Ndine, Yohane, mbale wanu, ndipo ngati mnzanu wokhulupirira Yesu, ndili nanu limodzi mu ufumu wa Mulungu, komanso m'masautso ndi m'kupirira kosatepatepa. Ndidaponyedwa pa chilumba cha Patimosi, chifukwa cha kulalika mau a Mulungu ndi kuchitira Yesu umboni. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Ine Yohane mʼbale wanu ndi mnzanu mʼmasautso ndi mu ufumu ndi mukupirira kwambiri, zomwe ndi zathu mwa Yesu, ndinali pa chilumba cha Patimo chifukwa cha Mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu. Onani mutuwo |
Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambire chilombo, kapena fano lake, nisanalandire lembalo pamphumi ndi padzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.