Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Afilipi 4:15 - Buku Lopatulika

15 Koma mudziwanso inu nokha, inu Afilipi, kuti m'chiyambi cha Uthenga Wabwino, pamene ndinachoka kutuluka mu Masedoniya, sunayanjane nane Mpingo umodzi wonse m'makhalidwe a chopereka ndi cholandira, koma inu nokha;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Koma mudziwanso inu nokha, inu Afilipi, kuti m'chiyambi cha Uthenga Wabwino, pamene ndinachoka kutuluka m'Masedoniya, sunayanjana nane Mpingo umodzi wonse m'makhalidwe a chopereka ndi cholandira, koma inu nokha;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Inu Afilipi, mukudziŵa inu nomwe kuti pamene ndidachoka ku Masedoniya, masiku oyamba aja akulalika Uthenga Wabwino, panalibe mpingo wina wogwirizana nane pa zoyenera kulipira kapena kulandira, koma inu nokha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Ndipo inu Afilipi mukudziwa kuti masiku oyambirira olalikira Uthenga Wabwino, nditachoka ku Makedoniya, panalibe mpingo ndi umodzi omwe umene unagwirizana nane pa nkhani yopereka ndi kulandira, kupatula inu.

Onani mutuwo Koperani




Afilipi 4:15
12 Mawu Ofanana  

Koma anati, Pali Yehova, amene ndiima pamaso pake, sindidzalandira kanthu. Ndipo anamkakamiza achilandire, koma anakana.


Koma Gehazi, mnyamata wa Elisa, munthu wa Mulungu, anati, Taona, mbuye wanga analekera Naamani uyu wa ku Aramu osalandira m'manja ake chimene anabwera nacho; pali Yehova, ndidzathamangira ndi kulandira kanthu kwa iye.


Ndipo anatuluka m'ndendemo, nalowa m'nyumba ya Lidia: ndipo pamene anaona abale, anawasangalatsa, namuka.


Pakuti kunakondweretsa a ku Masedoniya ndi Akaya kuchereza osauka a kwa oyera mtima a ku Yerusalemu.


Koma abale, ndifuna kuti muzindikire kuti zija za kwa ine zidachita makamaka kuthandizira Uthenga Wabwino;


ena atero ndi chikondi, podziwa kuti anandiika ndichite chokanira cha Uthenga Wabwino;


chifukwa cha chiyanjano chanu chakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;


monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndili nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'chisomo.


Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa